Luka 8:5 - Buku Lopatulika Anatuluka wofesa kukafesa mbeu zake; ndipo m'kufesa kwake zina zinagwa m'mbali mwa njira; ndipo zinapondedwa, ndi mbalame za m'mlengalenga zinatha kuzidya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anatuluka wofesa kukafesa mbeu zake; ndipo m'kufesa kwake zina zinagwa m'mbali mwa njira; ndipo zinapondedwa, ndi mbalame za m'mlengalenga zinatha kuzidya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Munthu wina adaapita kukafesa mbeu. Akufesa choncho, mbeu zina zidagwera m'njira. Zidapondedwa, ndipo mbalame zidazitolatola. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. Akufesa mbewuzo, zina zinagwa mʼmbali mwa njira; zinapondedwa, ndipo mbalame zamlengalenga zinadya. |
Inu ndinu mchere wa dziko lapansi; koma mcherewo ngati ukasukuluka, adzaukoleretsa ndi chiyani? Pamenepo sungakwanirenso kanthu konse, koma kuti ukaponyedwe kunja, nupondedwe ndi anthu.
Ndipo iwo ndiwo a m'mbali mwa njira mofesedwamo mau; ndipo pamene anamva, pomwepo akudza Satana nachotsa mau ofesedwa mwa iwo.
Ndipo pamene khamu lalikulu la anthu linasonkhana, ndi anthu a kumidzi yonse anafika kwa Iye, anati mwa fanizo:
Ndipo zina zinagwa pathanthwe; ndipo pakumera zinatofa msanga, chifukwa zinalibe mnyontho.
Mwa ichi tiyenera kusamaliradi zimene tidazimvazi kuti kapena tingatengedwe ndi kusiyana nazo.