Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 119:118 - Buku Lopatulika

118 Mupepula onse akusokera m'malemba anu; popeza chinyengo chao ndi bodza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

118 Mupepula onse akusokera m'malemba anu; popeza chinyengo chao ndi bodza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

118 Inu mumaŵakana anthu onse osamvera malamulo anu, zoonadi, kuchenjera kwao nkopandapake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

118 Inu mumakana onse amene amasochera kuchoka pa zophunzitsa zanu, pakuti chinyengo chawo ndi chopanda phindu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 119:118
19 Mawu Ofanana  

Ndinakufunani ndi mtima wanga wonse; ndisasokere kusiyana nao malamulo anu.


Munadzudzula odzikuza otembereredwa, iwo akusokera kusiyana nao malamulo anu.


Mundichotsere njira ya chinyengo; nimundipatse mwachifundo chilamulo chanu.


koma anabwerera m'mbuyo, nachita zosakhulupirika monga makolo ao, anapatuka ngati uta wolenda.


Zaka makumi anai mbadwo uwu unandimvetsa chisoni, ndipo ndinati, Iwo ndiwo anthu osokerera mtima, ndipo sadziwa njira zanga.


Chinyengo chili m'mitima ya oganizira zoipa; koma aphungu a mtendere amakondwa.


Chifukwa m'phiri limeneli dzanja la Yehova lidzakhalamo, ndipo Mowabu adzaponderezedwa pansi m'malo ake, monga udzu uponderezedwa padzala.


Iye adya phulusa; mtima wodzinyenga wampambutsa, kuti iye sangapulumutse moyo wake, pena kunena, Kodi simuli kunama m'dzanja langa lamanja?


Ndaponda ndekha mopondera mphesa, ndipo panalibe nane mmodzi wa mitundu ya anthu; inde ndinawaponda m'kukwiya kwanga, ndi kuwapondereza mu ukali wanga; ndi mwazi wa moyo wao unawazidwa pa zovala zanga; ndipo ndadetsa chofunda changa chonse.


Ndipo mudzapondereza oipa; pakuti adzakhala ngati mapulusa kumapazi anu, tsiku ndidzaikalo, ati Yehova wa makamu.


Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka kumitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza Yerusalemu kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira.


kuti muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo;


Asakunyengeni inu munthu ndi mau opanda pake, pakuti chifukwa cha izi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera.


Koma anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.


Sindinakulembereni chifukwa simudziwa choonadi, koma chifukwa muchidziwa, ndi chifukwa kulibe bodza lochokera kwa choonadi.


Ndipo moponderamo mphesa anamuponda kunja kwa mzinda, ndipo mudatuluka mwazi moponderamo mphesa, kufikira zapakamwa za akavalo, kufikira mastadiya chikwi ndi mazana asanu ndi limodzi.


ndi kuunika kwa nyali sikudzaunikiranso konse mwa iwe; ndi mau a mkwati ndi a mkwatibwi sadzamvekanso konse mwa iwe; pakuti otsatsa malonda anu anali omveka a m'dziko; pakuti ndi nyanga yako mitundu yonse inasokeretsedwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa