Luka 5:9 - Buku Lopatulika Pakuti chizizwo chidagwira iye, ndi onse amene anali naye, pa kusodzako kwa nsomba zimene anazikola; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti chizizwo chidagwira iye, ndi onse amene anali naye, pa kusodzako kwa nsomba zimene anazikola; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adaatero popeza kuti iye, pamodzi ndi onse amene anali naye, adaazizwa nako kuchuluka kwa nsomba zimene adaaphazo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye ndi anzake onse anadabwa ndi nsomba zimene anagwira, |
Ndipo anthu onse anadabwa, nalankhulana wina ndi mnzake, nanena, Mau amenewa ali otani? Chifukwa ndi ulamuliro ndi mphamvu angolamulira mizimu yonyansa, ndipo ingotuluka.
ndipo chimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedeo, amene anali anzake a Simoni. Ndipo Yesu anati kwa Simoni, Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.
Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mawondo ake a Yesu, nanena, Muchoke kwa ine, Ambuye, chifukwa ndine munthu wochimwa.