Ndipo adzanena, Undani, undani, konzani njira, chotsani chokhumudwitsa m'njira mwa anthu anga.
Luka 3:4 - Buku Lopatulika monga mwalembedwa m'buku la Yesaya mneneri, kuti, Mau a wofuula m'chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 monga mwalembedwa m'buku la Yesaya mneneri, kuti, Mau a wofuula m'chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Izi zidachitika monga zidaalembedwera m'buku la mneneri Yesaya kuti, “Liwu la munthu wofuula m'chipululu: akunena kuti, ‘Konzani mseu wodzadzeramo Ambuye, ongolani njira zoti adzapitemo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Monga analembera mʼbuku la Yesaya mneneri kuti: “Mawu a wofuwula mʼchipululu, konzani njira ya Ambuye, wongolani njira zake. |
Ndipo adzanena, Undani, undani, konzani njira, chotsani chokhumudwitsa m'njira mwa anthu anga.
Pitani, pitani pazipata; konzani njira ya anthu; undani, undani khwalala; chotsani miyala, kwezani mbendera ya anthu.
Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate ao; kuti ndisafike ndi kukantha dziko lionongeke konse.
Pakuti uyu ndiye ananenayo Yesaya mneneri, kuti, Mau a wofuula m'chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake.
Anati, Ndine mau a wofuula m'chipululu, Lungamitsani njira ya Mbuye, monga anati Yesaya mneneriyo.
Iyeyu anadza mwa umboni kudzachita umboni za kuunikaku, kuti onse akakhulupirire mwa iye.