Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 3:5 - Buku Lopatulika

5 Chigwa chilichonse chidzadzazidwa, ndipo phiri lililonse ndi mtunda uliwonse zidzachepsedwa; ndipo zokhota zidzakhala zolungama, ndipo njira za zigoloondo zidzakhala zosalala;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Chigwa chilichonse chidzadzazidwa, ndipo phiri lililonse ndi mtunda uliwonse zidzachepsedwa; ndipo zokhota zidzakhala zolungama, ndipo njira za zigoloondo zidzakhala zosalala;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Dzazani chigwa chilichonse, chepetsani phiri lililonse ndi mtunda uliwonse. Ongolani njira zokhotakhota, salazani njira zazigolowondo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Chigwa chilichonse chidzadzazidwa ndipo phiri lililonse ndi mtunda uliwonse zidzasalazidwa, misewu yokhotakhota idzawongoledwa, ndi njira zosasalala zidzasalazidwa.

Onani mutuwo Koperani




Luka 3:5
11 Mawu Ofanana  

Chigwa chilichonse chidzadzazidwa, ndipo phiri lililonse ndi chitunda chilichonse zidzachepetsedwa, ndipo zokhota zidzaongoledwa, ndipo zamakolokoto zidzasalala;


Ndipo ndidzayendetsa akhungu m'khwalala, limene iwo salidziwa, m'njira zimene iwo sazidziwa ndidzawatsogolera; ndidzawalitsa mdima m'tsogolo mwao, ndi kulungamitsa malo okhota. Zinthu izi Ine ndidzachita, ndipo sindidzawasiya.


Ndidzakutsogolera ndi kusalaza pokakala; ndidzathyolathyola zitseko zamkuwa, ndi kudula pakati akapichi achitsulo;


Ndipo ndidzasandutsa mapiri anga onse akhale njira, ndipo makwalala anga adzakwezeka.


Ndipo mitengo yonse yakuthengo idzadziwa kuti Ine Yehova ndatsitsa mtengo wosomphoka, ndakuza mtengo waung'ono, ndaumitsa mtengo wauwisi, ndi kuphukitsa mtengo wouma; Ine Yehova ndanena ndi kuchichita.


Koma mbale woluluka adzitamandire pa ukulu wake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa