Luka 21:3 - Buku Lopatulika Ndipo Iye anati, Zoonadi ndinena kwa inu, wamasiye uyu waumphawi anaikamo koposa onse; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye anati, Zoonadi ndinena kwa inu, wamasiye uyu waumphawi anaikamo koposa onse; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti mai wamasiye wosaukayu waponyamo koposa ena onseŵa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anati, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mkazi wamasiye wosaukayu wapereka zambiri kuposa ena onsewa. |
pakuti onse amenewa anaika mwa unyinji wao pa zoperekazo; koma iye mwa kusowa kwake anaikamo za moyo wake, zonse anali nazo.
Koma zoonadi ndinena kwa inu, kuti, Munali akazi amasiye ambiri mu Israele masiku ake a Eliya, pamene kunatsekedwa kumwamba zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, pamene panakhala njala yaikulu padziko lonselo;
Koma Ine ndinena ndi inu zoonadi, Kuli ena a iwo akuimirira pano, amene sadzalawatu imfa, kufikira kuti adzaona Ufumu wa Mulungu.
Ndipo Petro anatsegula pakamwa pake, nati, Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankho;
Pakuti zoonadi anasonkhanidwa m'mzinda muno Herode, ndi Pontio Pilato yemwe pamodzi ndi amitundu ndi anthu a Israele kumchitira choipa Mwana wanu wopatulika Yesu amene munamdzoza;
Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa.