Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 9:27 - Buku Lopatulika

27 Koma Ine ndinena ndi inu zoonadi, Kuli ena a iwo akuimirira pano, amene sadzalawatu imfa, kufikira kuti adzaona Ufumu wa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Koma Ine ndinena ndi inu zoonadi, Kuli ena a iwo akuimirira pano, amene sadzalawatu imfa, kufikira kuti adzaona Ufumu wa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Koma ndithu ndikunenetsa kuti alipo ena pompano omwe sadzafa asanaone Ufumu wa Mulungu utafika.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti ena mwa inu amene mwayima pano simudzalawa imfa musanaone ufumu wa Mulungu.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 9:27
11 Mawu Ofanana  

Indetu ndinena kwa inu, kuti alipo ena a iwo aima pano sadzalawa ndithu imfa, kufikira adzaona Mwana wa Munthu atadza mu ufumu wake.


Ndithu ndinena nanu, Sindidzamwanso chipatso cha mpesa, kufikira tsiku lijalo, limene ndidzamwa icho chatsopano mu Ufumu wa Mulungu.


Ndipo ananena nao, Ndithu ndinena ndi inu kuti, Alipo ena akuimirira pano, amene sadzalawa imfa konse, kufikira akaona Ufumu wa Mulungu utadza ndi mphamvu.


Ndipo anamuululira Mzimu Woyera kuti sadzaona imfa, kufikira adzaona Khristu wake wa Ambuye.


pakuti ndinena kwa inu, kuyambira tsopano Ine sindidzamwako chipatso cha mpesa, kufikira Ufumu wa Mulungu udzafika.


M'nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo.


Koma ndinena Ine choonadi ndi inu; kuyenera kwa inu kuti ndichoke Ine; pakuti ngati sindichoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzamtuma Iye kwa inu.


Pamenepo anatola miyala kuti amponye Iye; koma Yesu anabisala, natuluka mu Kachisi.


Koma timpenya Iye amene adamchepsa pang'ono ndi angelo, ndiye Yesu, chifukwa cha zowawa za imfa, wovala korona wa ulemerero ndi ulemu, kuti ndi chisomo cha Mulungu alawe imfa m'malo mwa munthu aliyense.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa