Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 9:26 - Buku Lopatulika

26 Pakuti aliyense amene adzachita manyazi chifukwa cha Ine ndi mau anga, Mwana wa Munthu adzachita manyazi chifukwa cha iye, pamene adzafika ndi ulemerero wake ndi wa Atate, ndi wa angelo oyera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Pakuti amene aliyense adzachita manyazi chifukwa cha Ine ndi mau anga, Mwana wa Munthu adzachita manyazi chifukwa cha iye, pamene adzafika ndi ulemerero wake ndi wa Atate, ndi wa angelo oyera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Pajatu munthu akamakana Ine ndiponso mau anga, nanenso Mwana wa Munthune ndidzamkana pamene ndidzabwera ndili ndi ulemerero wanga ndi wa Atate anga, ndi wa angelo oyera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Ngati wina aliyense achita nane manyazi ndi ndiponso mawu anga, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wake ndi mu ulemerero wa Atate ndi angelo oyera.

Onani mutuwo Koperani




Luka 9:26
30 Mawu Ofanana  

Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeze.


Mtsinje wamoto unayenda wotuluka pamaso pake, zikwizikwi anamtumikira, ndi unyinji wosawerengeka unaima pamaso pake, woweruza mlandu anakhalapo, ndi mabuku anatsegulidwa.


Pakuti Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate wake, pamodzi ndi angelo ake; ndipo pomwepo Iye adzabwezera kwa anthu onse monga machitidwe ao.


Koma pamene Mwana wa Munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pa chimpando cha kuwala kwake:


Yesu anati kwa iye, Mwatero, koma ndinenanso kwa inu, Kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa Munthu ali kukhala kudzanja lamanja la mphamvu, ndi kufika pa mitambo ya kumwamba.


Pakuti yense wakuchita manyazi chifukwa cha Ine, ndi cha mau anga mu mbadwo uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachitanso manyazi chifukwa cha iyeyu, pamene Iye adzafika nao angelo ake oyera, mu ulemerero wa Atate wake.


pakuti anakonda ulemerero wa anthu koposa ulemerero wa Mulungu.


Mungathe inu bwanji kukhulupirira, popeza mulandira ulemu wina kwa mnzake ndipo ulemu wakuchokera kwa Mulungu yekha simuufuna?


Ndipo anati, Kornelio kenturiyoyo, munthu wolungama ndi wakuopa Mulungu, amene mtundu wonse wa Ayuda umchitira umboni, anachenjezedwa ndi mngelo woyera kuti atumize nakuitaneni mumuke kunyumba yake, ndi kumvetsa mau anu.


Pakuti Uthenga Wabwino sundichititsa manyazi; pakuti uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu aliyense wakukhulupirira; kuyambira Myuda, ndiponso Mgriki.


Chifukwa chake ndisangalala m'mafooko, m'ziwawa, m'zikakamizo, m'mazunzo, m'zipsinjiko, chifukwa cha Khristu; pakuti pamene ndifooka, pamenepo ndili wamphamvu.


Koma kudzitamandira ine konsekonse, iai, koma mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene mwa Iye dziko lapansi lapachikidwira ine, ndi ine ndapachikidwira dziko lapansi.


Ndikuchitira umboni pamaso pa Mulungu, ndi Khristu Yesu, ndi angelo osankhika, kuti usunge izi kopanda kusankhiratu, wosachita kanthu monga mwa tsankho.


Chifukwa cha ichicho ndinamva zowawa izi; komatu sindichita manyazi; pakuti ndimdziwa Iye amene ndamkhulupirira, ndipo ndikopeka mtima kuti ali wa mphamvu ya kudikira chosungitsa changacho kufikira tsiku lijalo.


ngati tipirira, tidzachitanso ufumu ndi Iye: ngati timkana Iye, Iyeyunso adzatikana ife:


nawerenga tonzo la Khristu chuma choposa zolemera za Aejipito; pakuti anapenyerera chobwezera cha mphotho.


Chifukwa chake titulukire kwa Iye kunja kwa tsasa osenza tonzo lake.


Ndipo kwa iwo, Enoki, wachisanu ndi chiwiri kuyambira kwa Adamu, ananenera kuti, Taona, wadza Ambuye ndi oyera ake zikwi makumi,


Taonani, adza ndi mitambo; ndipo diso lililonse lidzampenya Iye, iwonso amene anampyoza; ndipo mafuko onse a padziko adzamlira Iye. Terotu. Amen.


Ndipo ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pake, ndipo sanapezedwe malo ao.


Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.


Iye amene apambana adzamveka motero zovala zoyera; ndipo sindidzafafaniza ndithu dzina lake m'buku la moyo, ndipo ndidzamvomereza dzina lake pamaso pa Atate wanga, ndi pamaso pa angelo ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa