Luka 2:1 - Buku Lopatulika Ndipo kunali masiku aja, kuti lamulo linatuluka kwa Kaisara Augusto kuti dziko lonse lokhalamo anthu lilembedwe; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali masiku aja, kuti lamulo linatuluka kwa Kaisara Augusto kuti dziko lonse lokhalamo anthu lilembedwe; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Masiku amenewo, Augusto, Mfumu ya ku Roma, adalamula kuti pakhale kalembera wa anthu a m'maiko ake onse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mʼmasiku amenewo Kaisara Augusto anapereka lamulo kuti kalembera achitike mʼdziko lonse la Aroma. |
Chifukwa chake mutiuze ife, muganiza chiyani? Kuloledwa kodi kupatsa msonkho kwa Kaisara, kapena iai?
Ndipo Uthenga uwu Wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.
Ndipo ndithu ndinena ndi inu, Ponse pamene padzalalikidwa Uthenga Wabwino kudziko lonse lapansi, ichinso chimene anachita mkazi uyu chidzanenedwa, chikhale chomkumbukira nacho.
Ndipo ananena nao, Mukani kudziko lonse lapansi, lalikirani Uthenga Wabwino kwa olengedwa onse.
kukalembedwa iye mwini pamodzi ndi Maria, wopalidwa naye ubwenzi; ndi uyu anali ndi pakati.
Ndipo pa chaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberio Kaisara, pokhala Pontio Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode chiwanga cha Galileya, ndi Filipo mbale wake chiwanga cha dziko la Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lisaniasi chiwanga cha Abilene;
Ndipo ananyamuka mmodzi wa iwo, dzina lake Agabu, nalosa mwa Mzimu, kuti padzakhala njala yaikulu padziko lonse lokhalamo anthu; ndiyo idadza masiku a Klaudio.
Pamenepo ngati ndili wochita zoipa, ngati ndachita kanthu kakuyenera imfa, sindikana kufa; koma ngati zinthuzi awa andinenera nazo zili zachabe, palibe mmodzi akhoza kundipereka kwa iwo. Nditulukira kwa Kaisara.
Koma pakunena Paulo ndi kuti, asungidwe, akatulukire kwa Augusto, ndinaweruza asungidwe iye kufikira ndikamtumiza kwa Kaisara.
Poyamba, ndiyamika Mulungu wanga mwa Yesu Khristu chifukwa cha inu nonse, chifukwa kuti mbiri ya chikhulupiriro chanu idamveka padziko lonse lapansi.