Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 9:4 - Buku Lopatulika

Koma nyama, m'mene muli moyo wake, ndiwo mwazi wake, musadye.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma nyama, m'mene muli moyo wake, ndiwo mwazi wake, musadye.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Koma pali chinthu chimodzi chokha chimene simuyenera kudya, ndicho nyama imene ikali ndi magazi. Ndaletsa poti magaziwo ndiwo moyo wake.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Koma musamadye nyama imene ikanali ndi magazi oyenda.

Onani mutuwo



Genesis 9:4
15 Mawu Ofanana  

Chifukwa chake unene nao, Atero Ambuye Yehova, Mumadyera kumodzi ndi mwazi, mumakwezera maso anu kumafano anu, ndi kukhetsa mwazi; ndipo kodi mudzakhala nalo dziko cholowa chanu?


Musamadya kanthu ndi mwazi wake; musamachita nyanga, kapena kuombeza ula.


Likhale lemba losatha m'mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse, musamadya kapena mafuta kapena mwazi.


Ndipo musamadya mwazi uliwonse, kapena wa mbalame, kapena wa nyama, m'nyumba zanu zonse.


koma kuti tilembere kwa iwo, kuti asale zonyansa za mafano, ndi dama, ndi zopotola, ndi mwazi.


chinatikomera ndi mtima umodzi, tisankhe anthu, ndi kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi okondedwa anthu Barnabasi ndi Paulo,


kuti musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama; ngati mudzisungitsa pa zimenezi, kudzakhala bwino kwa inu. Tsalani bwino.


Mwazi wao wokha musamadya; muziuthira panthaka ngati madzi.


Koma mulimbikepo ndi kusadya mwaziwo; popeza mwazi ndiwo moyo, nimusamadya moyo pamodzi ndi nyama yake.


Musamadya chinthu chilichonse chitafa chokha; muzipereka icho kwa mlendo ali m'mudzi mwanu, achidye ndiye; kapena uchigulitse kwa mlendo; popeza ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu. Musamaphika mwanawambuzi mu mkaka wa make.


Mwazi wake wokha musamadya; muuthire pansi ngati madzi.


Pakuti cholengedwa chonse cha Mulungu nchabwino, ndipo palibe kanthu kayenera kutayika, ngati kalandiridwa ndi chiyamiko;


Ndipo anthuwo anathamangira zowawanyazo, natenga nkhosa, ndi ng'ombe, ndi anaang'ombe, naziphera pansi; anthu nazidya zili ndi mwazi wao.