Genesis 7:6 - Buku Lopatulika Ndipo Nowa anali wa zaka mazana asanu ndi limodzi, pamene chigumula cha madzi chinali padziko lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Nowa anali wa zaka mazana asanu ndi limodzi, pamene chigumula cha madzi chinali pa dziko lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nowa anali wa zaka 600 pamene chigumulacho chidafika pa dziko lapansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene chigumula chinabwera pa dziko lapansi Nowa anali ndi zaka 600. |
Chaka cha mazana asanu ndi limodzi cha moyo wa Nowa, mwezi wachiwiri, tsiku la khumi ndi asanu ndi awiri la mwezi, tsiku lomwelo akasupe onse a madzi aakulu anasefuka, ndi mazenera a kumwamba anatseguka.
Ndipo panali chaka cha mazana asanu ndi limodzi kudza chimodzi, mwezi woyamba, tsiku loyamba mwezi, madzi anaphwa padziko lapansi; ndipo Nowa anachotsa tsindwi lake pachingalawa, nayang'ana, ndipo taonani, padauma padziko lapansi.