Genesis 8:13 - Buku Lopatulika13 Ndipo panali chaka cha mazana asanu ndi limodzi kudza chimodzi, mwezi woyamba, tsiku loyamba mwezi, madzi anaphwa padziko lapansi; ndipo Nowa anachotsa tsindwi lake pachingalawa, nayang'ana, ndipo taonani, padauma padziko lapansi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Ndipo panali chaka cha mazana asanu ndi limodzi kudza chimodzi, mwezi woyamba, tsiku loyamba mwezi, madzi anaphwa pa dziko lapansi; ndipo Nowa anachotsa chindwi lake pachingalawa, nayang'ana, ndipo taonani, padauma pa dziko lapansi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Nowa ali wa zaka 601, pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, madzi adaphweratu pa dziko lapansi. Nowa adatsekula zenera la chombo chija nayang'ana kunja, nkuwona kuti pansi pauma, Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Pofika tsiku loyamba la mwezi woyamba wa chaka chimene Nowa anakwanitsa zaka 601, madzi anawuma pa dziko lapansi. Ndipo Nowa anachotsa denga la chombo ndipo anaona kuti kunja kwawuma. Onani mutuwo |