Ndipo zinalowa kwa Nowa m'chingalawamo ziwiriziwiri zamoyo zonse, m'mene muli mpweya wa moyo.
Genesis 7:16 - Buku Lopatulika Zimene zinalowazo, zinalowa yamphongo ndi yaikazi zamoyo zonse, monga momwe Mulungu anamlamulira iye: ndipo Yehova anamtsekera iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Zimene zinalowazo, zinalowa yamphongo ndi yaikazi zamoyo zonse, monga momwe Mulungu anamlamulira iye: ndipo Yehova anamtsekera iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa monga Mulungu adaalamulira. Pomwepo Chauta adatseka pa khomo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye analowa nazo zazimuna ndi zazikazi monga mmene Mulungu anamulamulira. Kenaka Yehova anatseka pa khomo. |
Ndipo zinalowa kwa Nowa m'chingalawamo ziwiriziwiri zamoyo zonse, m'mene muli mpweya wa moyo.
Ndipo chigumula chinali padziko lapansi masiku makumi anai: ndipo madzi anachuluka natukula chingalawa, ndipo chinakwera pamwamba padziko lapansi.
zinalowa ziwiriziwiri kwa Nowa m'chingalawamo, yamphongo ndi yaikazi, monga momwe Mulungu anamlamulira Nowa.
Chifukwa chake sitidzachita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi, angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja.
Ndipo pamene iwo analikumuka kukagula, mkwati anafika; ndipo okonzekawo analowa naye pamodzi muukwati; ndipo anatseka pakhomo.
Pamene atauka mwini nyumba natseka pakhomo, ndipo inu mudzayamba kuima pabwalo, ndi kugogoda pachitseko, ndi kunena, Ambuye titsegulireni ife; ndipo Iye adzayankha nadzati ndi inu, Sindidziwa inu kumene muchokerako;
Mulungu wamuyaya ndiye mokhaliramo mwako; ndi pansipo pali manja osatha. Ndipo aingitsa mdani pamaso pako, nati, Ononga.
amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa chikhulupiriro, kufikira chipulumutso chokonzeka kukavumbulutsidwa nthawi yotsiriza.