Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 7:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo chigumula chinali padziko lapansi masiku makumi anai: ndipo madzi anachuluka natukula chingalawa, ndipo chinakwera pamwamba padziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo chigumula chinali pa dziko lapansi masiku makumi anai: ndipo madzi anachuluka natukula chingalawa, ndipo chinakwera pamwamba pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Chigumula chidagundika masiku makumi anai pa dziko lapansi. Madzi adayamba kukwera pa dziko lapansi, ndipo chombo chidayamba kuyandama.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Chigumula chinagwa pa dziko la pansi kwa masiku makumi anayi. Madzi anayamba kuchuluka ndipo ananyamula chombo chija ndi kuchiyandamitsa pamwamba pa dziko.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 7:17
5 Mawu Ofanana  

Ndipo mvula inali padziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku.


Zimene zinalowazo, zinalowa yamphongo ndi yaikazi zamoyo zonse, monga momwe Mulungu anamlamulira iye: ndipo Yehova anamtsekera iye.


Ndipo madzi anapambana, nachuluka ndithu padziko lapansi, ndipo chingalawa chinayandama pamadzi.


Pakuti akapita masiku asanu ndi awiri Ine ndidzavumbitsa mvula padziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku; ndi zinthu zamoyo zonse zomwe ndazipanga ndidzaziononga padziko lapansi.


ndiye amene amanga zipinda zake zosanja m'mwamba, nakhazika tsindwi lake padziko lapansi; Iye amene aitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira padziko; dzina lake ndiye Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa