Ndipo munali njala m'dzikomo, ndipo anatsikira Abramu ku Ejipito kukakhala kumeneko, chifukwa kuti njala inali yaikulu m'dziko m'menemo.
Genesis 43:1 - Buku Lopatulika Ndipo njala inakula m'dzikomo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo njala inakula m'dzikomo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Njala idakula kwambiri m'dziko la Kanani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Njala inakula kwambiri mʼdzikomo. |
Ndipo munali njala m'dzikomo, ndipo anatsikira Abramu ku Ejipito kukakhala kumeneko, chifukwa kuti njala inali yaikulu m'dziko m'menemo.
Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, Bwanji anaseka Sara, kuti, Kodi ndidzabala ine ndithu, ine amene ndakalamba?
Ndipo panali njala padzikopo, yoyenjezeka ndi njala yoyamba ija imene inali masiku a Abrahamu, ndipo Isaki ananka kwa Abimeleki mfumu ya Afilisti ku Gerari.
Ndipo ana aamuna a Israele anadza kudzagula mwa iwo amene anadzako, pakuti m'dziko la Kanani munali njala.
Ndipo panali pamene atatha kudya tirigu yense anatengayo ku Ejipito atate wao anati kwa iwo, Pitaninso, mukatigulire ife chakudya pang'ono.
Nati kwa Farao, Tafika kuti tikhale m'dzikomo; popeza palibe podyetsa zoweta za akapolo anu; pakuti njala yakula m'dziko la Kanani. Mulole tsopano akapolo anu akhale m'dziko la Goseni.
Ndipo muyankhe ndi kuti pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Kholo langa ndiye Mwaramu wakuti atayike, natsika kunka ku Ejipito, nagoneragonera komweko ali nao anthu pang'ono, nasandukako mtundu waukulu, wamphamvu, ndi wochuluka anthu ake;