Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 42:38 - Buku Lopatulika

38 Ndipo iye anati, Mwana wanga sadzatsikira ndi inu, chifukwa kuti mkulu wake wafa, ndipo watsala iye yekha; ngati choipa chikamgwera iye m'njira m'mene mupitamo, inu mudzatsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

38 Ndipo iye anati, Mwana wanga sadzatsikira ndi inu, chifukwa kuti mkulu wake wafa, ndipo watsala iye yekha; ngati choipa chikamgwera iye m'njira m'mene mupitamo, inu mudzatsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

38 Koma Yakobe adati, “Mwana wangayu sangapite nanu ai, paja mbale wake adamwalira, ndipo ndi yekhayu watsala. Mwina mwake angathe kuphedwa pa njira, ndipo ine m'mene ndakalambiramu, chisoni chotere chidzangonditsiriza.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

38 Koma Yakobo anati, “Mwana wanga sapita nanu kumeneko; mkulu wake anamwalira ndipo watsala yekha. Ngati choyipa chitamuchitikira pa ulendo mukupitawu, ndiye kuti ndi mmene ndakalambiramu inu mudzandipha ndi chisoni chotere.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 42:38
20 Mawu Ofanana  

Ndipo anazindikira nati, Ndiwo malaya a mwana wanga: wajiwa ndi chilombo: Yosefe wakadzulidwa ndithu.


Yakobo ndipo anang'amba malaya ake, na vala chiguduli m'chuuno mwake namlirira mwana wake masiku ambiri.


Ndipo ana aamuna ake onse ndi ana aakazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndilinkulirabe. Atate wake ndipo anamlirira.


Nati iwo, Akapolo anu ndife abale khumi, ana aamuna a munthu mmodzi m'dziko la Kanani; ndipo, taonani, wamng'ono ali ndi atate wathu lero; ndipo palibe mmodzi.


Ndipo Rubeni anati kwa atate wake, kuti, Muwaphe ana anga aamuna awiri ndikapanda kumbweza iye kwa inu; mumpereke iye m'manja mwanga, ndipo ine ndidzambwezanso kwa inu.


Koma Yakobo sanamtume Benjamini mphwake wa Yosefe, pamodzi ndi abale ake, chifukwa anati, Choipa chingam'gwere iye.


mutengenso mphwanu, nimunyamuke, mupitenso kwa munthu uja:


Ndipo tinati kwa mbuyanga, Tili ndi atate, munthu wokalamba, ndi mwana wa ukalamba wake wamng'ono; mbale wake wafa, ndipo iye yekha watsala wa amake, ndipo atate wake amkonda iye.


Ndipo ife tinati kwa mbuyanga, Mnyamata sangathei kumsiya atate wake; pakuti akamsiya atate wake, atate wake adzafa.


Chita mwa nzeru yako tsono, osalola mutu wake waimvi utsikire kumanda ndi mtendere.


Ichititsa mifunde yonyezimira pambuyo pake; munthu akadati pozama pali ndi imvi.


Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m'mbuyo.


Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi awiri, kapena tikakhala nayo mphamvudi zaka makumi asanu ndi atatu; koma teronso kukula kwao kumati chivuto ndi chopanda pake; pakuti kumapitako msanga ndipo tithawa ife tomwe.


Ndaona ntchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Pakuti yemwe Mulungu amuyesa wabwino ampatsa nzeru ndi chidziwitso ndi chimwemwe; koma wochimwa amlawitsa vuto la kusonkhanitsa ndi kukundika, kuti aperekere yemwe Mulungu amuyesa wabwino. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Ine ndinati, Pakati pa masiku anga ndidzalowa m'zipata za kunsi kwa manda; Ndazimidwa zaka zanga zotsala.


ngakhale mpaka mudzakalamba Ine ndine, ndipo ngakhale mpaka tsitsi laimvi, Ine ndidzakusenzani inu; ndalenga, ndipo ndidzanyamula; inde, ndidzasenza, ndipo ndidzapulumutsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa