Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 42:37 - Buku Lopatulika

37 Ndipo Rubeni anati kwa atate wake, kuti, Muwaphe ana anga aamuna awiri ndikapanda kumbweza iye kwa inu; mumpereke iye m'manja mwanga, ndipo ine ndidzambwezanso kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

37 Ndipo Rubeni anati kwa atate wake, kuti, Muwaphe ana anga amuna awiri ndikapanda kumbweza iye kwa inu; mumpereke iye m'manja mwanga, ndipo ine ndidzambwezanso kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

37 Rubeni adauza atate ake kuti, “Mungathe kudzapha ana anga aŵiri, ngati Benjamini sindidzabwera naye kwa inu. Mundipatse kuti ndimsamale ndine, ndipo ndidzabwera naye.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

37 Koma Rubeni anati kwa abambo ake, “Ngati sindidzabwera naye kwa inu, mudzaphe ana anga aamuna awiri. Muperekeni mʼmanja mwangamu ndipo ndidzamusamala ndi kubwera naye kwa inu.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 42:37
6 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo atate wao anati kwa iwo, Munandilanda ine ana; Yosefe palibe, Simeoni palibe, ndipo mudzachotsa Benjamini: zonse zimene zandigwera.


Ndipo iye anati, Mwana wanga sadzatsikira ndi inu, chifukwa kuti mkulu wake wafa, ndipo watsala iye yekha; ngati choipa chikamgwera iye m'njira m'mene mupitamo, inu mudzatsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda.


Ine ndidzakhala chikole, pa manja anga mudzamfunsa: ndikapanda kumbwezera kwa inu ndi kumuimitsa pamaso panu, chifukwa chake chidzakhala pa ine masiku onse:


Ndi ana aamuna a Rubeni: Hanoki, ndi Palu, ndi Hezironi, ndi Karimi.


Kodi Yehova adzakondwera nazo nkhosa zamphongo zikwi, kapena ndi mitsinje ya mafuta zikwi khumi? Kodi ndipereke mwana wanga woyamba chifukwa cha kulakwa kwanga, chipatso cha thupi langa chifukwa cha kuchimwa kwa moyo wanga?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa