Genesis 42:16 - Buku Lopatulika Tumizani mmodzi wa inu akatenge, adze naye mphwanu: ndipo inu mudzamangidwa kuti mau anu ayesedwe, ngati zoona zili mwa inu: penatu, pali moyo wa Farao, muli ozonda ndithu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tumizani mmodzi wa inu akatenge, adze naye mphwanu: ndipo inu mudzamangidwa kuti mau anu ayesedwe, ngati zoona zili mwa inu: penatu, pali moyo wa Farao, muli ozonda ndithu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tumani mmodzi mwa inu kuti apite akamtenge. Ena nonse otsalanu mukhale m'ndende ndithu, mpaka mau anuŵa atsimikizike, tiwone ngati mukunena zoona. Apo ai, ndithu pali Farao, inuyo ndinu azondi basi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tumizani mmodzi wa inu akamutenge mʼbale wanuyo ndipo ena nonsenu musungidwa mʼndende, kuti titsimikize ngati zimene mukunenazi ndi zoona. Apo ayi, pali Farao ndithu, inu ndinu akazitape!” |
Koma akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni mbuye wao, Kodi muganiza kuti Davide alemekeza atate wanu, popeza anakutumizirani osangalatsa? Kodi Davide sanatumize anyamata ake kwa inu, kuti ayang'ane mzindawo ndi kuuzonda ndi kuupasula?
Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, ali ku Sitimu, anatuma amuna awiri mosadziwika kukazonda, ndi kuti, Mukani, mulipenye dzikolo, ndi ku Yeriko. Ndipo anamuka nalowa m'nyumba ya mkazi wadama, dzina lake Rahabi, nagona momwemo.