Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 42:15 - Buku Lopatulika

15 Mudzayesedwa ndi ichi, pali moyo wa Farao, simudzatuluka muno, koma akadze kuno mphwanu ndiko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Mudzayesedwa ndi ichi, pali moyo wa Farao, simudzatuluka muno, koma akadze kuno mphwanu ndiko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Tsono ndikuyesani motere; ndikulumbira kuti pali Farao! Inuyo simuchoka, mpaka mng'ono wanuyo atabwera kuno.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Ndiye ndikuyesani motere: Ine ndikulumbira pali Farao ndithu, inuyo simudzachoka malo ano mpaka wotsirizayo atabwera kuno.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 42:15
19 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anati kwa iwo, Iai, koma mwadzera kuti muone usiwa wa dziko.


Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Ndicho chimene ndinakunenani inu, kuti, Ndinu ozonda.


Tumizani mmodzi wa inu akatenge, adze naye mphwanu: ndipo inu mudzamangidwa kuti mau anu ayesedwe, ngati zoona zili mwa inu: penatu, pali moyo wa Farao, muli ozonda ndithu.


koma mukatenge mphwanu kudza naye kwa ine, kuti atsimikizidwe mau anu ndipo simudzafa. Ndipo anachita chomwecho.


kuti, Munthu mwini dziko, ananena ndi ife mwankhalwe, natiyesa ife ozonda dziko.


idzani naye mphwanu kwa ine, ndipo ndidzadziwa kuti simuli ozonda koma anthu oona: chomwecho ndidzakubwezerani inu mbale wanu, ndipo mudzachita malonda m'dziko muno.


Ndipo Yosefe anaona abale ake, ndipo anazindikira iwo, koma anadziyesetsa kwa iwo ngati mlendo, nanena kwa iwo mwankhanza: ndipo anati kwa iwo, Mufuma kuti inu? Nati iwo, Ku dziko la Kanani kudzagula chakudya.


Ndipo Yuda ananena ndi iye kuti, Munthu uja anatilimbitsira mau kuti, simudzaonanso nkhope yanga, koma mphwanu akhale ndi inu ndiko.


Koma mukapanda kumtuma iye sititsika; pakuti munthu uja anati kwa ife, Simudzaona nkhope yanga, ngati mphwanu sali ndi inu.


Ndipo ngakhale ati, Pali Yehova; komatu alumbira monama.


Bwanji ndidzakhululukira iwe? Pamenepo ana ako andisiya Ine, nalumbira pa iyo yosati milungu; pamene ndinakhutitsa iwo, anachita chigololo, nasonkhana pamodzi m'nyumba za adama.


Muziopa Yehova Mulungu wanu; ndi kutumikira Iyeyu; ndipo polumbira muzitchula dzina lake.


Koma makamaka, abale anga, musalumbire, kungakhale kutchula kumwamba kapena dziko, kapena lumbiro lina lililonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iai wanu akhale iai; kuti mungagwe m'chiweruziro.


Ndipo mkaziyo ananena, Mbuye wanga, pali moyo wanu, zoonadi ine ndine mkazi uja ndidaima pano ndi inu, ndi kupemphera kwa Yehova.


Ndipo pamene Saulo anaona Davide alikutulukira kwa Mfilistiyo, iye anati kwa Abinere, kazembe wa khamu la nkhondo, Abinere, mnyamata uyu ndi mwana wa yani? Nati Abinere, Pali moyo wanu, mfumu, ngati ndidziwa.


Ndipo Davide analumbiranso nati, Atate wako adziwatu kuti wandikomera mtima; nati, Yonatani asadziwe ichi, kuti angamve chisoni; koma pali Yehova, ndiponso pali moyo wako, pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazi limodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa