Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 42:1 - Buku Lopatulika

Ndipo anaona Yakobo kuti mu Ejipito munali tirigu, nati Yakobo kwa ana ake aamuna, Chifukwa chanji mulinkuyang'anana?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anaona Yakobo kuti m'Ejipito munali tirigu, nati Yakobo kwa ana ake amuna, Chifukwa chanji mulinkuyang'anana?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yakobe atamva kuti ku Ejipito ndiko kuli tirigu, adafunsa ana ake kuti, “Chifukwa chiyani mukungokhala osachitapo kanthu?

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yakobo atamva kuti ku Igupto kuli tirigu, anati kwa ana ake, “Nʼchifukwa chiyani mukungoyangʼanana wina ndi mnzake?

Onani mutuwo



Genesis 42:1
13 Mawu Ofanana  

Ndipo zinayamba kufika zaka zisanu ndi ziwiri za njala, monga ananena Yosefe; ndipo munali njala m'maiko monse; koma m'dziko lonse la Ejipito munali chakudya.


Ndipo maiko onse anafika ku Ejipito kudzagula tirigu kwa Yosefe: chifukwa njala inakula m'dziko lonse lapansi.


Ndipo iye anati, Taonani, ndamva kuti mu Ejipito muli tirigu, mutsikireko mutigulire kumeneko; kuti tikhale ndi moyo, tisafe.


Ndipo iye ataona chimenechi, ananyamuka, nathawa kupulumutsa moyo, nafika ku Beereseba wa ku Yuda, nasiya mnyamata wake pamenepo.


Nyamukani, mlandu ndi wanu; ndipo ife tili nanu; limbikani, chitani.


Ndipo anthu onse anaona mabingu ndi zimphezi, ndi liu la lipenga ndi phiri lilikufuka; ndipo pamene anthu anaziona, ananjenjemera, naima patali.


Ndipo akapitao a ana a Israele anaona kuti kudawaipira, pamene ananena, Musamachepetsa njerwa zanu, ntchito ya tsiku pa tsiku lake.


Tikhaliranji ife? Tasonkhanani, tilowe m'mizinda yamalinga, tikhale chete m'menemo; pakuti Yehova Mulungu wathu watikhalitsa ife chete, natipatsa ife madzi a ndulu timwe, pakuti tamchimwira Yehova.


Pamene Efuremu anaona nthenda yake, ndi Yuda bala lake, Efuremu anamuka kwa Asiriya, natumiza kwa mfumu Yarebu; koma iye sakhoza kukuchiritsani, kapena kupoletsa bala lanu.


Koma pakumva Yakobo kuti muli tirigu mu Ejipito, anatuma makolo athu ulendo woyamba.


koma pena, pakuona kuti anaikiza kwa ine Uthenga Wabwino wa kusadulidwa, monga kwa Petro Uthenga Wabwino wa mdulidwe


Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Tauka, wagweranji pankhope pako chotere?