Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 7:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Tauka, wagweranji pankhope pako chotere?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Tauka, wagweranji pankhope pako chotere?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Chauta adamuuza Yoswa kuti, “Dzuka, chifukwa chiyani wagwada pansi chotere?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Koma Yehova anati kwa Yoswa, “Imirira! Chifukwa chiyani wagwada pansi chotere?

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 7:10
7 Mawu Ofanana  

golide, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, nzosawerengeka; nyamuka, nuchite, Yehova akhale nawe.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ufuuliranji kwa Ine? Lankhula ndi ana a Israele kuti aziyenda.


Ndipo Yehova anati kwa Yoswa,


Israele wachimwa, nalakwiranso chipangano changa, ndinawalamuliracho; natengakonso choperekedwacho; anabanso, nanyenganso, nachiika pakati pa akatundu ao.


Akadzamva ichi Akanani ndi okhala m'dziko onse, adzatizinga ndi kuduliratu dzina lathu padziko lapansi; ndipo mudzachitiranji dzina lanu lalikulu?


Ndipo Samuele anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.


Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Iwe ukuti ulire chifukwa cha Saulo nthawi yotani, popeza Ine ndinamkana kuti asakhale mfumu ya Israele? Dzaza nyanga yako ndi mafuta, numuke, ndidzakutumiza kwa Yese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa