Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 41:57 - Buku Lopatulika

57 Ndipo maiko onse anafika ku Ejipito kudzagula tirigu kwa Yosefe: chifukwa njala inakula m'dziko lonse lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

57 Ndipo maiko onse anafika ku Ejipito kudzagula tirigu kwa Yosefe: chifukwa njala inakula m'dziko lonse lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

57 Anthu ankafika ku Ejipito kuchokera ku mbali zonse za dziko lapansi, kudzagula tirigu kwa Yosefe, chifukwa njala inali itakula koopsa konsekonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

57 Anthu ankabwera ku Igupto kuchokera ku mayiko ena onse kudzagula tirigu kwa Yosefe, chifukwa njala inafika poyipa kwambiri pa dziko lonse lapansi.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 41:57
11 Mawu Ofanana  

Ndipo munali njala m'dzikomo, ndipo anatsikira Abramu ku Ejipito kukakhala kumeneko, chifukwa kuti njala inali yaikulu m'dziko m'menemo.


Ndipo zinayamba kufika zaka zisanu ndi ziwiri za njala, monga ananena Yosefe; ndipo munali njala m'maiko monse; koma m'dziko lonse la Ejipito munali chakudya.


Ndipo njala inali padziko lonse lapansi; ndipo Yosefe anatsegula nkhokwe zonse nagulitsa Aejipito: ndipo njala inakula m'dziko la Ejipito.


Ndipo anaona Yakobo kuti mu Ejipito munali tirigu, nati Yakobo kwa ana ake aamuna, Chifukwa chanji mulinkuyang'anana?


Ndipo ana aamuna a Israele anadza kudzagula mwa iwo amene anadzako, pakuti m'dziko la Kanani munali njala.


Ndipo Yosefe anali wolamulira dziko; ndiye amene anagulitsa kwa anthu onse a m'dziko; ndipo anafika abale ake a Yosefe, namweramira pansi, nkhope zao pansi.


Ndipo njala inakula m'dzikomo.


Ndipo Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse anazipeza m'dziko la Ejipito ndi m'dziko la Kanani, za tirigu amene anagula; ndipo Yosefe anapereka ndalama kunyumba ya Farao.


Koma inu, munandipangira ine choipa; koma Mulungu anachipangira chabwino, kuti kuchitike monga lero, kupulumutsa amoyo anthu ambiri.


kuti linganene dziko limene mudatitulutsako, Popeza Yehova sanakhoze kuwalowetsa m'dziko limene adanena nao, ndi popeza anadana nao, anawatulutsa kuti awaphe m'chipululu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa