Yeremiya 8:14 - Buku Lopatulika14 Tikhaliranji ife? Tasonkhanani, tilowe m'mizinda yamalinga, tikhale chete m'menemo; pakuti Yehova Mulungu wathu watikhalitsa ife chete, natipatsa ife madzi a ndulu timwe, pakuti tamchimwira Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Tikhaliranji ife? Tasonkhanani, tilowe m'midzi yamalinga, tikhale chete m'menemo; pakuti Yehova Mulungu wathu watikhalitsa ife chete, natipatsa ife madzi a ndulu timwe, pakuti tamchimwira Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Anthu amati, “Chifukwa chiyani tikungokhala? Tiyeni tonse pamodzi tithaŵire ku mizinda yamalinga, tikafere komweko. Chauta, Mulungu wathu, wagamula kuti tiyenera kufa, watimwetsa madzi aululu pakuti tamchimwira. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Koma amati, “Tikukhala pano chifukwa chiyani? Tiyeni tonse pamodzi tithawire ku mizinda yotetezedwa ndi kukafera kumeneko. Pakuti Yehova Mulungu wathu watsimikiza kuti tiyenera kufa. Watipatsa madzi aululu kuti timwe, chifukwa tamuchimwira. Onani mutuwo |