Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 40:1 - Buku Lopatulika

Ndipo panali zitapita izi, wopereka chikho wa mfumu ya Aejipito ndi wophika mkate wake anamchimwira mbuye wao mfumu ya Aejipito.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo panali zitapita izi, wopereka chikho wa mfumu ya Aejipito ndi wophika mkate wake anamchimwira mbuye wao mfumu ya Aejipito.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Patapita kanthaŵi, munthu woperekera vinyo pamodzi ndi wopanga buledi ku nyumba ya mfumu ya ku Ejipito, adalakwira mbuyao mfumu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Patapita nthawi, woperekera zakumwa ndi wopanga buledi a ku nyumba kwa mfumu ya ku Igupto analakwira mbuye wawoyo.

Onani mutuwo



Genesis 40:1
10 Mawu Ofanana  

ndipo chikho cha Farao chinali m'dzanja langa: ndipo ndinatenga mphesa, ndi kufinyira m'chikho cha Farao ndi kupereka chikho m'dzanja la Farao.


akali masiku atatu Farao adzatukula mutu wako, nadzabwezera iwe ntchito yako; ndipo udzapereka chikho cha Farao m'dzanja lake, monga kale lomwe m'mene unali wopereka chikho chake.


Pamene wophika mkate anaona kuti kumasulira kwake kunali kwabwino, iye anati kwa Yosefe, Inenso ndinalimkulota, ndipo, taonani, malichero atatu a mikate yoyera anali pamutu panga;


Ndipo Farao anakwiyira akulu ake awiriwo wamkulu wa opereka chikho, ndi wamkulu wa ophika mkate.


Ndipo analota maloto onse awiri, yense loto lake, usiku umodzi, yense monga mwa kumasulira kwa loto lake, wopereka chikho ndi wophika mkate wa mfumu ya Aejipito, amene anamangidwa m'kaidi.


Pamenepo wopereka chikho wamkulu anati kwa Farao, kuti, Ine ndidzakumbukira zochimwa zanga lero.


Ambuye, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mupambanitse kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera chifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu chakumwa chake.


Usiku uja tulo tidamwazikira mfumu, niti abwere nalo buku la mbiri, naliwerenga pamaso pa mfumu.