Kaini ndipo ananena ndi Abele mphwake. Ndipo panali pamene anali kumunda, Kaini anamuukira Abele mphwake, namupha.
Genesis 4:25 - Buku Lopatulika Ndipo Adamu anadziwanso mkazi wake; ndipo anabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Seti, chifukwa anati iye, Mulungu wandilowezera ine mbeu ina m'malo mwa Abele amene Kaini anamupha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Adamu anadziwanso mkazi wake; ndipo anabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Seti: Chifukwa, nati iye, Mulungu wandilowezera ine mbeu ina m'malo mwa Abele amene Kaini anamupha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adamu adakhalanso ndi Heva mkazi wake, ndipo adatenga pathupi nabala mwana. Tsono Hevayo adati, “Mulungu wandipatsa mwana woloŵa m'malo mwa Abele uja amene adaphedwa ndi Kaini.” Mwanayo adamutcha Seti. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Adamu anagonanso malo amodzi ndi mkazi wake, ndipo anabereka mwana wamwamuna namutcha Seti, kutanthauza kuti, “Mulungu wandipatsa mwana wina mʼmalo mwa Abele, popeza Kaini anamupha.” |
Kaini ndipo ananena ndi Abele mphwake. Ndipo panali pamene anali kumunda, Kaini anamuukira Abele mphwake, namupha.