kuti ana aamuna a Mulungu anayang'ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.
Genesis 39:7 - Buku Lopatulika Ndipo panali zitapita izi, kuti mkazi wa mbuyake anamyang'anira maso Yosefe: ndipo mkaziyo anati, Gona ndi ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali zitapita izi, kuti mkazi wa mbuyake anamyang'anira maso Yosefe: ndipo mkaziyo anati, Gona ndi ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Patapita kanthaŵi, mkazi wa bwana wake adayamba kusirira Yosefe. Tsono mkaziyo adauza Yosefeyo kuti, “Bwanji ugone nane.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Patapita kanthawi, mkazi wa mbuye wake anayamba kusirira Yosefe nati, “Bwanji ugone nane!” |
kuti ana aamuna a Mulungu anayang'ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.
Ndipo pamene anabwera nato pafupi kuti adye, iye anamgwira, nanena naye, Idza nugone nane, mlongo wanga.
Nzeru idzakupulumutsa kwa mkazi wachiwerewere, kwa mkazi wachilendo wosyasyalika ndi mau ake;
Pakuti ukayamba ndi mkazi wadama, udzamaliza ndi nyenyeswa; ndipo mkazi wa mwini amasaka moyo wa mtengowapatali.
Ndipo mvula yakanidwa, ndipo panalibe mvula ya masika; ndipo unali ndi nkhope ya mkazi wadama, unakana manyazi.
Unamanga chiunda chako pa mphambano zilizonse, ndipo unanyansitsa kukongola kwako, ndi kutukula mapazi ako kwa yense wopitako, ndi kuchulukitsa chigololo chako.
M'mwemo usiyana konse ndi akazi ena m'chigololo chako; pakuti palibe wokutsata kuchita nawe chigololo; popezanso uwalipira, koma sakupatsa iwe mphotho; potero usiyana nao konse ena.
koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.
okhala nao maso odzala ndi chigololo, osakhoza kuleka uchimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero;
Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi.