Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 38:10 - Buku Lopatulika

Koma chimene iye anachita chinali choipa pamaso pa Yehova, ndipo anamupha iyenso.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma chimene iye anachita chinali choipa pamaso pa Yehova, ndipo anamupha iyenso.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono zimene ankachitazo zidaipira Chauta ndipo Chauta adamlanganso ndi imfa.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Zimene ankachitazi zinayipira Yehova. Choncho anamulanganso ndi imfa.

Onani mutuwo



Genesis 38:10
13 Mawu Ofanana  

Ndi ana aamuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m'dziko la Kanani. Ndi ana aamuna a Perezi ndiwo Hezironi ndi Hamuli.


Ndipo pakutuluka malirowo, Davide anatumiza munthu namtenga afike kwao kunyumba yake; ndipo iyeyo anakhala mkazi wake nambalira mwana wamwamuna. Koma Yehova anaipidwa ndi chinthu chimene Davide adachita.


Nafuulira kwa Yehova, nati, Yehova Mulungu wanga, kodi mwamgwetsera choipa mkazi wamasiye amene ndikhala naye, kumphera mwanake?


Ana a Yuda ndiwo Eri, ndi Onani, ndi Sela; Batisuwa Mkanani anambalira atatu amenewa. Koma Eri mwana woyamba wa Yuda anali woipa pamaso pa Yehova, ndi Iye anamupha.


Ndipo Mulungu anaipidwa nacho chinthuchi, chifukwa chake Iye anakantha Israele.


Wochimwa adzakankhidwa m'kuipa kwake; koma wolungama akhulupirirabe pomwalira.


kuti Yehova angaone kukondwa kwako, ndi kukuyesa koipa, ndi kuleka kumkwiyira.


Koma ndinatuma kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndinauka mamawa ndi kuwatuma, ndi kuti, Musachitetu chonyansa ichi ndidana nacho.


Ndipo Hagai mthenga wa Yehova, mu uthenga wa Yehova ananena ndi anthu, ndi kuti, Ine ndili nanu, ati Yehova.


Ndipo anthu anaipa, namadandaula m'makutu a Yehova; ndipo pamene Yehova anamva anapsa mtima; ndi moto wa Yehova unayaka pakati pao, nunyeketsa ku chilekezero cha chigono.


Pamenepo Balamu anati kwa mthenga wa Yehova, Ndachimwa, popeza sindinadziwe kuti munaima mondiletsa m'njira; ndipo tsopano, ngati chikuipirani, ndibwerera.


Ana aamuna a Yuda, ndiwo Eri ndi Onani; ndipo Eri ndi Onani anamwalira m'dziko la Kanani.


Munthu akachimwira munthu mnzake oweruza adzaweruza mlandu wake; koma ngati munthu achimwira Yehova, adzampembedzera ndani? Koma ngakhale adatero, iwo aja anakhalabe osamvera mau a atate wao, chifukwa Yehova adati adzawaononga.