Ndipo panali pamene Yosefe anafika kwa abale ake, anamvula Yosefe malaya ake, malaya amwinjiro amene anavala iye;
Genesis 37:3 - Buku Lopatulika Koma Israele anamkonda Yosefe koposa ana ake onse, pakuti anali mwana wa ukalamba wake; ndipo anamsokera iye malaya amwinjiro. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Israele anamkonda Yosefe koposa ana ake onse, pakuti anali mwana wa ukalamba wake; ndipo anamsokera iye malaya amwinjiro. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Israele ankakonda Yosefe kupambana ana ake ena onse, popeza kuti anali mwana wake wapaukalamba. Adamsokera mkanjo wautali wamanja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Israeli ankakonda Yosefe koposa ana ake ena onse, chifukwa anali mwana wobadwa muukalamba wake. Ndipo anamusokera mkanjo wa manja aatali. |
Ndipo panali pamene Yosefe anafika kwa abale ake, anamvula Yosefe malaya ake, malaya amwinjiro amene anavala iye;
natumiza malaya amwinjiro, nadza nao kwa atate ao: ndipo anati, Siwa tawatola; muzindikire tsono ngati ndi malaya a mwana wanu, kapena ndi ena.
Ndipo iye anavala chovala cha mawangamawanga, popeza ana aakazi a mfumu okhala anamwali amavala zotere. Ndipo mnyamata wake anamtulutsa, napiringidza chitseko atapita iye.
Ndipo unatengako zovala zako, ndi kudzimangira misanje ya mawangamawanga, ndi kuchitapo chigololo; zotere sizinayenere kufika kapena kuchitika.
Kodi sanapeze, sanagawe zofunkha? Namwali, anamwali awiri kwa munthu aliyense. Chofunkha cha nsalu za mawangamawanga kwa Sisera; chofunkha cha nsalu za mawangamawanga, za maluwa, nsalu za mawangamawanga, za maluwa konsekonse, kwa chofunkha cha khosi lake.