Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 37:2 - Buku Lopatulika

2 Mibadwo ya Yakobo ndi iyi; Yosefe anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri analinkudyetsa zoweta pamodzi ndi abale ake; ndipo anali mnyamata pamodzi ndi ana a Biliha, ndi ana aamuna a Zilipa, akazi a atate wake; ndipo Yosefe anamfotokozera atate wake mbiri yao yoipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Mibadwo ya Yakobo ndi iyi; Yosefe anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri analinkudyetsa zoweta pamodzi ndi abale ake; ndipo anali mnyamata pamodzi ndi ana a Biliha, ndi ana amuna a Zilipa, akazi a atate wake; ndipo Yosefe anamfotokozera atate wake mbiri yao yoipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Mbiri ya banja la Yakobe ndi iyi: Pamene Yosefe anali mnyamata wa zaka 17, ankaŵeta nkhosa ndi mbuzi pamodzi ndi abale ake, ana a Biliha aja ndi a Zilipa, akazi aang'ono a bambo wake. Tsono Yosefeyo ankauza bambo wake zoipa zimene ankachita abale akewo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri ya banja la Yakobo ndi iyi: Yosefe, mnyamata wa zaka 17 ankaweta nkhosa ndi abale ake, pamodzi ndi ana a Biliha ndi Zilipa, akazi a abambo ake. Tsono Yosefe ankabwera kudzawuza abambo ake zoyipa za abale ake.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 37:2
17 Mawu Ofanana  

Mibadwo ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti, ndi iyi; kwa iwo ndipo kunabadwa ana aamuna, chitapita chigumula chija.


Imeneyo ndiyo mibadwo yao ya zakumwamba ndi dziko lapansi, pamene zinalengedwa, tsiku lomwe Yehova Mulungu anapanga dziko lapansi ndi zakumwamba.


Ndipo Rakele anampatsa iye Biliha mdzakazi wake akhale mkazi wake; ndipo Yakobo analowa kwa iye.


Pamene Leya anaona kuti analeka kubala, anatenga Zilipa mdzakazi wake, nampatsa iye kwa Yakobo kuti akhale mkazi wake.


Ndipo panali pamene Israele anakhala m'dzikomo, Rubeni anamuka nagona ndi Biliha, mkazi wamng'ono wa atate wake: ndipo Israele anamva. Ana aamuna a Yakobo anali khumi ndi awiri:


Ndipo Yosefe anali wa zaka makumi atatu pamene iye anaima pamaso pa Farao mfumu ya Aejipito. Ndipo Yosefe anatuluka pamaso pa Farao, napitapita padziko lonse la Ejipito.


Ndipo Yosefe anazindikira abale ake, koma iwo sanamzindikire iye.


Zaka ziwirizi muli njala m'dziko muno; ndipo zatsala zaka zisanu, zopanda kulima kapena kusenga.


Mudzati, Akapolo anu akhala oweta ng'ombe chiyambire ubwana wathu kufikira tsopano, ife ndi atate athu; kuti mukhale m'dziko la Goseni; chifukwa abusa onse anyansira Aejipito.


Ili ndi buku la mibadwo ya Adamu. Tsiku lomwe Mulungu analenga munthu anamlenga m'chifanizo cha Mulungu;


Mibadwo ya Nowa ndi iyi: Nowa anali munthu wolungama ndi wangwiro m'mibadwo yake; Nowa anayendabe ndi Mulungu.


Dziko lapansi silingathe kudana ndi inu; koma Ine lindida popeza Ine ndilichitira umboni, kuti ntchito zake zili zoipa.


Pakuti zinamveka kwa ine za inu, abale anga, ndi iwo a kwa Koloe, kuti pali makani pakati pa inu.


Pakutitu poyamba posonkhana inu mu Mpingo, ndimva kuti pakhala malekano mwa inu; ndipo ndivomereza penapo.


Kwamveka ndithu kuti kuli chigololo pakati panu, ndipo chigololo chotere chonga sichimveka mwa amitundu, kuti wina ali naye mkazi wa atate wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa