Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 32:16 - Buku Lopatulika

Ndipo anazipereka zimenezo m'manja a anyamata ake, gulu pa lokha gulu pa lokha: ndipo anati kwa anyamata ake, Taolokani patsogolo panga, tachitani danga pakati pa magulu, lina ndi lina.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anazipereka zimenezo m'manja a anyamata ake, gulu pa lokha gulu pa lokha: ndipo anati kwa anyamata ake, Taolokani patsogolo panga, tachitani danga pakati pa magulu, lina ndi lina.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Gulu lililonse la zoŵeta adalipatsa mnyamata wosamala, ndipo adaŵauza onsewo kuti, “Inu mutsogoleko, ndipo poyenda ndi magulu a zoŵeta, muzisiya mpata pakati pa gulu lililonse.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iye anazipereka kwa antchito ake kuti azikuse, gulu lililonse pa lokha, ndipo anati kwa antchito akewo, “Tsogolani ndipo muonetsetse kuti pali mpata pakati pa gulu ndi gulu linzake.”

Onani mutuwo



Genesis 32:16
9 Mawu Ofanana  

ngamira zamkaka makumi atatu ndi ana ao, ng'ombe zazikazi makumi anai, zazimuna khumi, abulu aakazi makumi awiri ndi ana khumi.


Ndipo anauza wotsogolera kuti, Pamene akomana nawe mkulu wanga Esau ndi kufunsa iwe kuti, Ndiwe yani, umuka kuti? Za yani zimenezi patsogolo pako?


ndiponso muziti, Ndiponso, taonani, kapolo wanu Yakobo ali pambuyo pathu. Pakuti anati, Ndidzampembedzera iye ndi mphatso imene ipita patsogolo panga, pambuyo pake ndidzaona nkhope yake; kapena adzandilandira ine.


Wodala munthu wakuchitira chifundo, nakongoletsa; adzalimbika nao mlandu wake poweruzidwa.


kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakutchinjiriza;


Pakuti Mulungu wake amlangiza bwino namphunzitsa.


Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.


Nati kwa anyamata ake, Nditsogolereni; onani ndidza m'mbuyo mwanu. Koma sanauze mwamuna wake Nabala.