Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 32:20 - Buku Lopatulika

20 ndiponso muziti, Ndiponso, taonani, kapolo wanu Yakobo ali pambuyo pathu. Pakuti anati, Ndidzampembedzera iye ndi mphatso imene ipita patsogolo panga, pambuyo pake ndidzaona nkhope yake; kapena adzandilandira ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 ndiponso muziti, Ndiponso, taonani, kapolo wanu Yakobo ali pambuyo pathu. Pakuti anati, Ndidzampembedzera iye ndi mphatso imene ipita patsogolo panga, pambuyo pake ndidzaona nkhope yake; kapena adzandilandira ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Muzikati, ‘Ndiponso mtumiki wanu Yakobe ali m'mbuyo mwathumu.’ ” Yakobe ankaganiza kuti, “Ndimtsitsa mtima ndi mphatso zimene ndamtumizirazi, ndipo ndikakumana naye, mwina adzandilandira bwino.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Muzikanena kuti, ‘Wantchito wanu Yakobo akubwera mʼmbuyo mwathumu.’ ” Popeza anaganiza kuti, “Ndidzamutsitsa mtima ndi mphatso ndazitsogozazi. Apo tsono ndikadzakumana naye, mwina adzandilandira bwino.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 32:20
14 Mawu Ofanana  

Ndipo anauzanso wachiwiri ndi wachitatu, ndi onse anatsata magulu, kuti, Muzinena kwa Esau chotero, pamene mukomana naye:


Momwemo naolotsa mphatso patsogolo pake: ndipo iye yekha anagona usiku womwewo pachigono.


Ndipo Israele atate wao anati kwa iwo, Ngati chomwecho tsopano chitani ichi: tengani zipatso za m'dziko muno m'zotengera zanu, mumtengere munthu uja mphatso, mafuta amankhwala pang'ono, ndi uchi pang'ono, zonunkhira ndi mure, ndi mfula, ndi katungurume;


Pamenepo anyamata ake anati kwa iye, Taonani, tidamva ife kuti mafumu a nyumba ya Israele ndi mafumu achifundo; tiyeni tivale chiguduli m'chuuno mwathu, ndi zingwe pamitu pathu, titulukire kwa mfumu ya Israele, kapena adzakusungirani moyo.


Munthu wozaza aputa makani; koma wosakwiya msanga atonthoza makangano.


Mkwiyo wa mfumu ndi mithenga ya imfa; wanzeru adzaukhulula.


Mtulo wa munthu umtsegulira njira, numfikitsa pamaso pa akulu.


Mphatso ya m'tseri ipembedza mkwiyo, ndi mtulo wa pamfunga ukali wolimba.


Sadzalabadira chiombolo chilichonse, sadzapembedzeka ngakhale uchulukitsa malipo.


Kaya, akatembenuka Mulungu, ndi kuleka kubwera ku mkwiyo wake waukali, kuti tisatayike.


wolangiza iwo akutsutsana mofatsa; ngati kapena Mulungu awapatse iwo chitembenuziro, kukazindikira choonadi,


Chifukwa chake muzipanga zifanizo za mafundo anu, ndi zifanizo za mbewa zanu zimene ziipitsa dziko; ndipo muchitire ulemu Mulungu wa Israele; kuti kapena adzaleza dzanja lake pa inu, ndi pa milungu yanu, ndi padziko lanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa