Genesis 23:7 - Buku Lopatulika Ndipo anauka Abrahamu naweramira anthu a m'dzikomo, ana a Hiti. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anauka Abrahamu naweramira anthu a m'dzikomo, ana a Hiti. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Abrahamu adaimirira nkuŵeramira anthuwo, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Abrahamu anayimirira naweramira anthu a dziko la Hiti aja |
Ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anaona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati,
Ndipo anadza ku Sodomu madzulo amithenga awiri; ndipo Loti anakhala pa chipata cha Sodomu, ndipo Loti anaona iwo, nauka kuti akakomane nao, ndipo anaweramitsa pansi nkhope yake.
Mutimvere ife mfumu, ndinu kalonga wamkulu pakati pa ife; muike wakufa wanu m'manda mwathu mosankhika: palibe munthu yense wa ife adzakaniza manda ake, kuti muike wakufa wanu.
Ndipo ananena nao, kuti, Ngati mukandivomereza kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso, mundimvere ine, mundinenere ine kwa Efuroni mwana wake wa Zohari,
Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye:
Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa;