Ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi atatu kudza zisanu ndi chimodzi, pamene Hagara anambalira Abramu Ismaele.
Genesis 21:5 - Buku Lopatulika Ndipo Abrahamu anali wa zaka zana limodzi pamene anambadwira iye Isaki mwana wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abrahamu anali wa zaka zana limodzi pamene anambadwira iye Isaki mwana wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abrahamu nkuti ali wa zaka 100 pamene Isakiyo adabadwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abrahamu anali ndi 100 pamene mwana wake Isake anabadwa. |
Ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi atatu kudza zisanu ndi chimodzi, pamene Hagara anambalira Abramu Ismaele.
Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro.
Ndipo Abrahamu adagwa nkhope pansi, naseka, nati m'mtima mwake, Kodi mwana adzabadwa kwa iye amene ali wa zaka zana? Kodi Sara wa zaka makumi asanu ndi anai adzabala?
Ndipo Abrahamu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, pamene anadulidwa m'khungu lake.
Pambuyo pake ndipo anabadwa mphwake ndipo dzanja lake linagwira chitendeni cha Esau, ndi dzina lake linatchedwa Yakobo: ndipo Isaki anali wa zaka makumi asanu ndi limodzi pamene mkazi wake anabala iwo.
Atembereredwe munthu amene anatengera mau kwa atate wanga, kuti, Mwana wamwamuna anakubadwira iwe; ndi kumsekeretsatu iye.
Ndipo iye osafooka m'chikhulupiriro sanalabadire thupi lake, ndilo longa ngati lakufa pamenepo, (pokhala iye ngati zaka makumi khumi), ndi mimba ya Sara idaumanso;