Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 25:26 - Buku Lopatulika

26 Pambuyo pake ndipo anabadwa mphwake ndipo dzanja lake linagwira chitendeni cha Esau, ndi dzina lake linatchedwa Yakobo: ndipo Isaki anali wa zaka makumi asanu ndi limodzi pamene mkazi wake anabala iwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Pambuyo pake ndipo anabadwa mphwake ndipo dzanja lake linagwira chitende cha Esau, ndi dzina lake linatchedwa Yakobo: ndipo Isaki anali wa zaka makumi asanu ndi limodzi pamene mkazi wake anabala iwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Pobadwa mng'ono wake, dzanja lake linali litagwira chidendene cha Esau. Motero adamutcha Yakobe. Pamene ana ameneŵa ankabadwa, nkuti Isaki ali wa zaka 60.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Kenaka mʼbale wake anabadwa atagwira chidendene cha Esau; choncho anamutcha Yakobo. Isake anali ndi zaka 60 pamene Rebeka anabereka mapasawa.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 25:26
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anali wa zaka zana limodzi pamene anambadwira iye Isaki mwana wake.


ndipo Isaki anali wa zaka makumi anai pamene anakwata Rebeka, mwana wamkazi wa Betuele Mwaramu wa ku Padanaramu, mlongo wake wa Labani Mwaramu.


Ndipo iye anati, Kodi si ndicho chifukwa anamutcha dzina lake Yakobo? Kuti wandinyenga ine kawiri aka; analanda ukulu wanga ndipo taonani, tsopano walanda mdalitso wanga. Ndipo anati, Kodi simunandisungire ine mdalitso?


Ndipo masiku a Isaki anali zaka zana limodzi kudza makumi asanu ndi atatu.


Ndipo Abrahamu anabala Isaki. Ana a Isaki: Esau, ndi Israele.


M'mimba anagwira kuchitendeni cha mkulu wake, ndipo atakula mphamvu analimbana ndi Mulungu;


inde, analimbana ndi wamthenga nampambana; analira, nampembedza Iye; anampeza Iye ku Betele, ndi kumeneko Iye analankhula ndi ife;


Ndakukondani, ati Yehova; koma inu mukuti, Mwatikonda motani? Esau si mkulu wake wa Yakobo kodi? Ati Yehova; ndipo ndinakonda Yakobo;


Pamenepo Mose anatumiza amithenga ochokera ku Kadesi kumuka kwa mfumu ya Edomu, ndi kuti, Atero mbale wanu Israele, Mudziwa zowawa zonse zinatigwera;


Ndipo anampatsa iye chipangano cha mdulidwe; ndipo kotero Abrahamu anabala Isaki, namdula tsiku lachisanu ndi chitatu; ndi Isaki anabala Yakobo, ndi Yakobo anabala makolo aakulu aja khumi ndi awiri.


Ana obadwa nao a mbadwo wachitatu alowe m'msonkhano wa Yehova.


Ndi kwa Isaki ndinapatsa Yakobo ndi Esau, ndipo ndinampatsa Esau phiri la Seiri likhale lakelake; koma Yakobo ndi ana ake anatsikira kunka ku Ejipito.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa