Koma akakhala nanu mlendo, nakonzera Yehova Paska, adulidwe amuna ake onse, ndipo pamenepo asendere kuuchita; nakhale ngati wobadwa m'dziko; koma wosadulidwa aliyense asadyeko.
Genesis 21:4 - Buku Lopatulika Ndipo Abrahamu anamdula mwana wake wamwamuna Isaki pamene anali wa masiku ake asanu ndi atatu, monga Mulungu anamlamulira iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abrahamu anamdula mwana wake wamwamuna Isaki pamene anali wa masiku ake asanu ndi atatu, monga Mulungu anamlamulira iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abrahamu adamuumbala mwanayo ali wa masiku asanu ndi atatu, monga momwe Mulungu adaalamulira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Isake atakwanitsa masiku asanu ndi atatu, Abrahamu anamuchita mdulidwe monga Mulungu anamulamulira. |
Koma akakhala nanu mlendo, nakonzera Yehova Paska, adulidwe amuna ake onse, ndipo pamenepo asendere kuuchita; nakhale ngati wobadwa m'dziko; koma wosadulidwa aliyense asadyeko.
Ndipo panali tsiku lachisanu ndi chitatu iwo anadza kudzadula kamwanako; ndipo akati amutche dzina la atate wake Zekariya.
Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa.
Ndipo pamene panakwanira masiku asanu ndi atatu akumdula Iye, anamutcha dzina lake Yesu, limene anatchula mngeloyo asanalandiridwe Iye m'mimba.
Ndipo anampatsa iye chipangano cha mdulidwe; ndipo kotero Abrahamu anabala Isaki, namdula tsiku lachisanu ndi chitatu; ndi Isaki anabala Yakobo, ndi Yakobo anabala makolo aakulu aja khumi ndi awiri.