Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 12:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu adule khungu la mwanayo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu adule khungu la mwanayo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu mwanayo aumbalidwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, mwanayo achite mdulidwe.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 12:3
15 Mawu Ofanana  

Uzitero nazo ng'ombe zako, ndi nkhosa zako; masiku asanu ndi atatu akhale ndi amai wake; tsiku lachisanu ndi chitatu uzimpereka kwa Ine.


Ndipo akhale m'mwazi wa kumyeretsa kwake masiku makumi atatu kudza atatu; asakhudze kanthu kopatulika, kapena kulowa m'malo opatulika, kufikira adakwanira masiku a kumyeretsa kwake.


Ndipo kudetsedwa kwa kukha kwake ndiko: ngakhale chakukhacho chituluka m'thupi mwake, ngakhale chaleka m'thupi mwake, ndiko kumdetsa kwake.


Ndipo panali tsiku lachisanu ndi chitatu iwo anadza kudzadula kamwanako; ndipo akati amutche dzina la atate wake Zekariya.


Ndipo pamene panakwanira masiku asanu ndi atatu akumdula Iye, anamutcha dzina lake Yesu, limene anatchula mngeloyo asanalandiridwe Iye m'mimba.


Ndipo anadza ena akutsika ku Yudeya, nawaphunzitsa abale, nati, Mukapanda kudulidwa monga mwambo wa Mose, simungathe kupulumuka.


Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;


Ndipo ichi ndinena: Lamulo, limene linafika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi atatu, silifafaniza pangano lolunzika kale ndi Mulungu, kuliyesa lonjezanolo lachabe.


Ndichitanso umboni kwa munthu yense wolola amdule, kuti ali wamangawa kuchita chilamulo chonse.


Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudulani mtima wanu, ndi mtima wa mbeu zanu, kuti mukonde Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, kuti mukhale ndi moyo.


wodulidwa tsiku lachisanu ndi chitatu, wa mbadwo wa Israele, wa fuko la Benjamini, Muhebri wa mwa Ahebri; monga mwa lamulo, Mfarisi;


amenenso munadulidwa mwa Iye ndi mdulidwe wosachitika ndi manja, m'mavulidwe a thupi, mu mdulidwe wa Khristu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa