Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 12:2 - Buku Lopatulika

2 Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Akaima mkazi, nakabala mwana wamwamuna, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri; monga masiku ake akukhala padera, podwala iye, adzakhala wodetsedwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Akaima mkazi, nakabala mwana wamwamuna, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri; monga masiku ake akukhala padera, podwala iye, adzakhala wodetsedwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Uza Aisraele kuti mkazi akakhala ndi pakati, nabala mwana wamwamuna, adzakhala woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri, monga pa nthaŵi yake yakusamba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Awuze Aisraeli kuti, ‘Mkazi akakhala woyembekezera, nabala mwana wa mwamuna, mkaziyo adzakhala wodetsedwa kwa masiku asanu ndi awiri, ngati pa masiku ake akusamba.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 12:2
14 Mawu Ofanana  

Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.


Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.


Ndipo Davide anatumiza mithenga, namtenga iye; iye nabwera kwa iye, ndipo anagona naye, pakuti adachoka mumsambo; ndipo anabwereranso kunyumba yake.


Adzatulutsa choyera m'chinthu chodetsa ndani? Nnena mmodzi yense.


Munthu nchiyani kuti akhale woyera, wobadwa ndi mkazi kuti akhale wolungama?


Potero munthu akhala bwanji wolungama kwa Mulungu? Kapena wobadwa ndi mkazi akhala woyera bwanji?


Onani, ndinabadwa m'mphulupulu, ndipo mai wanga anandilandira m'zoipa.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,


Koma akabala mwana wamkazi, akhale wodetsedwa masabata awiri, monga umo amakhala padera; ndipo adzakhala m'mwazi wa kumyeretsa kwake masiku makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi.


Ndipo ngati mkazi ali ndi nthenda yakukha, ndi kukha kwake nkwa mwazi m'thupi mwake, akhale padera masiku asanu ndi awiri; ndipo aliyense amkhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Usamasendera kwa mkazi kumvula pokhala ali padera chifukwa cha kudetsedwa kwake.


Kapena akakhudza chodetsa cha munthu, ndicho chodetsa chilichonse akhala wodetsedwa nacho, ndipo chidambisikira; koma pochizindikira akhala wopalamula:


Ndipo pamene anakwanira masiku a kukonza kwao, monga mwa chilamulo cha Mose, iwo anakwera naye kunka ku Yerusalemu, kukamsonyeza Iye kwa Ambuye,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa