Ndipo Lameki anadzitengera yekha akazi awiri: dzina lake la wina ndi Ada, dzina lake la mnzake ndi Zila.
Genesis 2:24 - Buku Lopatulika Chifukwa chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake mwamuna amasiya atate ndi amai, ndipo amaphatikana ndi mkazi wake, choncho aŵiriwo amakhala thupi limodzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼchifukwa chake, mwamuna amasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake ndipo awiriwo amakhala thupi limodzi. |
Ndipo Lameki anadzitengera yekha akazi awiri: dzina lake la wina ndi Ada, dzina lake la mnzake ndi Zila.
Tamvera, mwana wamkaziwe, taona, tatchera khutu lako; uiwalenso mtundu wako ndi nyumba ya atate wako;
Mkazi wodekha ndiye korona wa mwamuna wake; koma wochititsa manyazi akunga chovunditsa mafupa a mwamunayo.
ameneyo, m'mene anafika, naona chisomo cha Mulungu, anakondwa; ndipo anawadandaulira onse, kuti atsimikize mtima kukhalabe ndi Ambuye;
Pakuti mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wake wamoyo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamulo la mwamunayo.
Muziopa Yehova Mulungu wanu; mumtumikire Iyeyo; mummamatire Iye, ndi kulumbira pa dzina lake.
Chifukwa chake nditi akwatiwe amasiye aang'ono, nabale ana, naweruzire nyumba, osapatsa chifukwa kwa mdaniyo chakulalatira;