Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Bwera kwa wakuka wako, udzichepetse wekha pamanja pake.
Genesis 16:6 - Buku Lopatulika Koma Abramu anati kwa Sarai, Taona, mdzakazi wako ali m'dzanja lako, umchitire iye chimene chikukomera m'maso mwako. Ndipo Sarai anamsautsa iye, ndipo anathawa kumaso kwake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Abramu anati kwa Sarai, Taona, mdzakazi wako ali m'dzanja lako, umchitire iye chimene chikukomera m'maso mwako. Ndipo Sarai anamsautsa iye, ndipo anathawa kumaso kwake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abramu adayankha kuti, “Iyeyu ndi mdzakazi wako, ndipo ali mu ulamuliro wako. Chita naye chilichonse chomwe ufuna.” Choncho Sarai adayamba kuzunza Hagara, mpaka Hagarayo adathaŵa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abramu anati, “Wantchito wakoyu ali mʼmanja mwako. Chita naye chilichonse chimene ukuganiza kuti ndi chokukomera.” Tsono Sarai anazunza Hagara mpaka anathawa. |
Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Bwera kwa wakuka wako, udzichepetse wekha pamanja pake.
Ndipo mnyamatayo anatenga ngamira khumi za mbuyake, namuka: chifukwa kuti chuma chonse cha mbuyake chinali m'dzanja lake: ndipo anachoka namuka ku Mesopotamiya, kumzinda wa Nahori.
Pamene Farao anachimva ichi, anafuna kupha Mose. Koma Mose anathawa pankhope pa Farao, nakhala m'dziko la Midiyani; nakhala pansi pachitsime.
Ngati mkulu akukwiyira, usasiye malo ako; chifukwa chifatso chipembedza utachimwa kwambiri.
Ndipo mfumu Zedekiya anati, Taonani, ali m'manja mwanu; pakuti mfumu singathe kuchita kanthu kotsutsana nanu.
Ndipo tsopano, taonani, tili m'dzanja lanu; monga muyesa chokoma ndi choyenera kutichitira ife, chitani.
Momwemonso amuna inu, khalani nao monga mwa chidziwitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu, monganso wolowa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.