Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 2:15 - Buku Lopatulika

15 Pamene Farao anachimva ichi, anafuna kupha Mose. Koma Mose anathawa pankhope pa Farao, nakhala m'dziko la Midiyani; nakhala pansi pachitsime.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Pamene Farao anachimva ichi, anafuna kupha Mose. Koma Mose anathawa pankhope pa Farao, nakhala m'dziko la Midiyani; nakhala pansi pachitsime.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Tsono Farao atamva, adayesetsa kuti aphe Mose, koma Mose adathaŵa nakakhala ku dziko la Midiyani. Ali kumeneko, tsiku lina adakhala pansi pafupi ndi chitsime.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Farao atamva zimenezi anafuna kuti aphe Mose, koma Mose anathawa ndipo anapita kukakhala ku Midiyani. Ali kumeneko, tsiku lina anakhala pansi pafupi ndi chitsime.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 2:15
17 Mawu Ofanana  

Ndipo anagwaditsa ngamira zake kunja kwa mzinda, ku chitsime cha madzi nthawi yamadzulo, nthawi yotuluka akazi kudzatunga madzi.


Ndipo anambalira iye Zimirani ndi Yokisani ndi Medani, ndi Midiyani, ndi Isibaki, ndi Suwa.


Ana a Midiyani: Efa, ndi Efere, ndi Hanoki, ndi Abida, ndi Elida. Onse amenewa ndi ana a Ketura.


Ndipo anayang'ana, taonani, chitsime m'dambo, ndipo, taonani, magulu atatu a nkhosa alinkugona kumeneko: pakuti pachitsimepo anamwetsa nkhosa; ndipo mwala wa pakamwa pa chitsime unali waukulu.


Ndipo anachoka ku Midiyani nafika ku Parani, natenga anthu a ku Parani pamodzi nao, nafika ku Ejipito kwa Farao mfumu ya Aejipito, ameneyo anampatsa nyumba, namnenera zakudya, nampatsako dziko.


ndi dzina la mnzake ndiye Eliyezere; pakuti anati, Mulungu wa kholo langa anakhala thandizo langa nandilanditsa ku lupanga la Farao.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose mu Midiyani, Muka, bwerera kunka ku Ejipito; pakuti adafa anthu onse amene anafuna moyo wako.


Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.


Ndinaona mahema a Kusani ali mkusauka; nsalu zotchinga za dziko la Midiyani zinanjenjemera.


Koma pamene angakuzunzeni inu m'mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israele, kufikira Mwana wa Munthu atadza.


ndipo pamenepo panali chitsime cha Yakobo. Ndipo Yesu, popeza analema ndi ulendo wake, motero anakhala pachitsime.


Ndipo Mose anathawa pa mau awa, nakhala mlendo m'dziko la Midiyani; kumeneko anabala ana aamuna awiri.


Ndi chikhulupiriro anasiya Ejipito, wosaopa mkwiyo wa mfumu; pakuti anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa