Genesis 16:5 - Buku Lopatulika5 Ndipo Sarai anati kwa Abramu, kusauka kwanga kukhale pa iwe: ndakupatsa iwe mdzakazi wanga pamtima pako; ndipo pakuona kuti anatenga pakati anandipeputsa ine m'maso mwake: Yehova aweruze pakati pa iwe ndi ine. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Ndipo Sarai anati kwa Abramu, kusauka kwanga kukhale pa iwe: ndakupatsa iwe mdzakazi wanga pamtima pako; ndipo pakuona kuti anatenga pakati anandipeputsa ine m'maso mwake: Yehova aweruze pakati pa iwe ndi ine. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Tsiku lina Sarai adauza Abramu kuti, “Cholakwa chimenechi chakuti Hagara akundinyoza, chili pa inu. Ine ndidakupatsani mdzakazi ameneyu, ndipo kuyambira paja adatenga pathupipa, wakhala akundinyoza. Chauta ndiye aweruze kuti tiwone wolakwa ndani pakati pathu.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Pamenepo Sarai anati kwa Abramu, “Inu ndinu amene mwandiputira nkhanza zikundichitikirazi. Ndinakupatsani wantchito wanga wamkazi kuti akhale mkazi wanu, ndiye tsopano wayamba kundinyoza ine chifukwa wadziwa kuti ndi woyembekezera. Yehova ndiye amene aweruze pakati pa inu ndi ine.” Onani mutuwo |