Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 16:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo analowa kwa Hagara, ndipo iye anatenga pakati. Pamene anaona kuti anatenga pakati, anapeputsa wakuka wake m'maso mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo analowa kwa Hagara, ndipo iye anatenga pakati. Pamene anaona kuti anatenga pakati, anapeputsa wakuka wake m'maso mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Abramu ataloŵana ndi Hagara, Hagarayo adatenga pathupi ndipo pompo Hagara adayamba kudzitama, namanyoza Sarai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Abramu atalowana ndi Hagara, Hagara uja anatenga mimba. Pamene Hagara anadziwa kuti anali woyembekezera anayamba kunyoza mbuye wake Sarai.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 16:4
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Sarai mkazi wake wa Abramu anatenga Hagara mdzakazi wake wa ku Ejipito, Abramu atakhala m'dziko la Kanani zaka khumi, nampereka iye kwa Abramu mwamuna wake, kuti akhale mkazi wake.


Ndipo Sarai anati kwa Abramu, kusauka kwanga kukhale pa iwe: ndakupatsa iwe mdzakazi wanga pamtima pako; ndipo pakuona kuti anatenga pakati anandipeputsa ine m'maso mwake: Yehova aweruze pakati pa iwe ndi ine.


Woyamba ndipo anati kwa wamng'ono, Atate wathu akalamba, ndipo palibe padziko lapansi mwamuna amene adzalowa kwa ife monga amachita padziko lonse lapansi:


Ndipo Sara anaona mwana wake wamwamuna wa Hagara Mwejipito, amene anambalira Abrahamu, alinkuseka.


Ndipo Rakele anampatsa iye Biliha mdzakazi wake akhale mkazi wake; ndipo Yakobo analowa kwa iye.


Ndipo kunali pamene likasa la Yehova linafika m'mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo, analikupenya pazenera, naona mfumu Davide alikuvina ndi kusewera pamaso pa Yehova, nampeputsa mumtima mwake.


chifukwa cha mkazi wodedwa wokwatidwa; ndi mdzakazi amene adzalandira cholowa cha mbuyake.


Koma izi, abale, ndadziphiphiritsira ndekha ndi Apolo, chifukwa cha inu, kuti mwa ife mukaphunzire kusapitirira zimene zilembedwa; kuti pasakhale mmodzi wodzitukumulira mnzake ndi kukana wina.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa