Ndipo kuyamba kwake kwa ufumu wake kunali Babiloni, ndi Ereke, ndi Akadi, ndi Kaline, m'dziko la Sinara.
Genesis 11:9 - Buku Lopatulika Chifukwa chake anatcha dzina lake Babiloni pakuti kumeneko Yehova anasokoneza chinenedwe cha dziko lonse lapansi; kuyambira pamenepo Yehova anabalalitsa iwo padziko lonse lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake anatcha dzina lake Babele; pakuti kumeneko Yehova anasokoneza chinenedwe cha dziko lonse lapansi; kuyambira pamenepo Yehova anabalalitsa iwo pa dziko lonse lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho mzinda umenewo adautcha Babele, chifukwa choti kumeneko Chauta adasokoneza chilankhulo cha anthu onse. Ndipo kuchokera kumeneko adaŵamwaza anthuwo pa dziko lonse lapansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼchifukwa chake mzindawo unatchedwa Babeli, popeza Yehova anasokoneza chiyankhulo cha anthu onse. Powachotsa kumeneko, Yehova anawabalalitsira pa dziko lonse lapansi. |
Ndipo kuyamba kwake kwa ufumu wake kunali Babiloni, ndi Ereke, ndi Akadi, ndi Kaline, m'dziko la Sinara.
Amenewa ndi ana aamuna a Hamu monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao.
Kwa Eberi ndipo kunabadwa ana aamuna awiri; dzina la wina ndi Pelegi; chifukwa kuti m'masiku ake dziko lapansi linagawanikana; dzina la mphwake ndi Yokotani.
Amenewo ndipo anagawa zisumbu za amitundu m'maiko mwao, onse amene monga mwa chinenedwe chao; ndi mwa mabanja ao, ndi m'mitundu yao.
ndipo ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi, atapangiratu nyengo zao, ndi malekezero a pokhala pao;
Chifukwa chake, ngati Mpingo wonse akasonkhane pamodzi, ndi onse akalankhule malilime, ndipo akalowemo anthu osaphunzira kapena osakhulupirira, kodi sadzanena kuti mwayaluka?