Ndipo kuyamba kwake kwa ufumu wake kunali Babiloni, ndi Ereke, ndi Akadi, ndi Kaline, m'dziko la Sinara.
Genesis 11:2 - Buku Lopatulika Ndipo panali pamene anayendayenda ulendo kum'mawa, anapeza chigwa m'dziko la Sinara, ndipo anakhala kumeneko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali pamene anayendayenda ulendo kum'mawa, anapeza chigwa m'dziko la Sinara, ndipo anakhala kumeneko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atasamukira chakuvuma, adakafika ku chigwa ku dziko la Sinara kumene adakhazikika. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene anthu amapita chakummawa anapeza chigwa ku dziko la Sinara nakhazikikako. |
Ndipo kuyamba kwake kwa ufumu wake kunali Babiloni, ndi Ereke, ndi Akadi, ndi Kaline, m'dziko la Sinara.
Chifukwa chake anatcha dzina lake Babiloni pakuti kumeneko Yehova anasokoneza chinenedwe cha dziko lonse lapansi; kuyambira pamenepo Yehova anabalalitsa iwo padziko lonse lapansi.
Ndipo Loti anasankha chigwa chonse cha Yordani; ndipo Loti anachoka ulendo wake kunka kum'mawa: ndipo analekana wina ndi mnzake.
Ndipo panali masiku a Amurafere mfumu ya Sinara, ndi Ariyoki mfumu ya Elasara, ndi Kedorilaomere mfumu ya Elamu, ndi Tidala mfumu ya Goimu,
Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti Ambuye adzabweza kachiwiri ndi dzanja lake anthu ake otsala ochokera ku Asiriya, ndi ku Ejipito, ndi ku Patirosi, ndi ku Kusi, ndi ku Elamu, ndi ku Sinara, ndi ku Hamati, ndi ku zisumbu za m'nyanja.
Ndipo Ambuye anapereka Yehoyakimu mfumu ya Yuda, m'dzanja lake, pamodzi ndi zipangizo zina za m'nyumba ya Mulungu, namuka nazo iye kudziko la Sinara, kunyumba ya mulungu wake, nalonga zipangizozo m'nyumba ya chuma cha mulungu wake.
Ndipo anati kwa ine, Kummangira nyumba m'dziko la Sinara; kuti amuike efayo, namkhazikeko pamalo kwake.