Ndipo Mulungu anati, Pakhale zounikira pathambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka;
Genesis 1:20 - Buku Lopatulika Ndipo anati Mulungu, Madzi abale zochuluka zamoyo zoyendayenda, ndi mbalame ziuluke pamwamba padziko lapansi ndi pamlengalenga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati Mulungu, Madzi abale zochuluka zamoyo zoyendayenda, ndi mbalame ziuluke pamwamba pa dziko lapansi ndi pamlengalenga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zitatero Mulungu adati, “M'nyanja mukhale zamoyo zambirimbiri, ndipo pakhale mbalame zouluka mu mlengalenga.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mulungu anati, “Mʼmadzi mukhale zamoyo zochuluka ndipo mbalame ziwuluke mlengalenga pamwamba pa dziko lapansi.” |
Ndipo Mulungu anati, Pakhale zounikira pathambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka;
Mulungu ndipo adalenga zinsomba zazikulu ndi zoyendayenda zamoyo zakuchuluka m'madzi mwa mitundu yao, ndi mbalame zamapiko, yonse monga mwa mtundu wake: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.
Mulungu ndipo anadalitsa zimenezo, nati, Zibalane, zichuluke, zidzaze madzi a m'nyanja, ndi mbalame zichuluke padziko lapansi.
ndiponso ndapatsa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi zokwawa zonse za dziko lapansi m'mene muli moyo, therere laliwisi lonse likhale chakudya: ndipo kunatero.
Ndipo Mulungu anapanga thambo, nalekanitsa madzi anali pansi pathambolo ndi madzi anali pamwamba pathambolo; ndipo kunatero.
Ndipo Yehova Mulungu anaumba ndi nthaka zamoyo zonse za m'thengo, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga; ndipo anapita nazo kwa Adamu kuti aone maina omwe adzazitcha; ndipo maina omwe onse anazitcha Adamu zamoyo zonse, omwewo ndiwo maina ao.
Ndipo zinafa zamoyo zonse zoyenda padziko lapansi, zouluka, ndi nyama, ndi zamoyo, ndi zokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi, ndi anthu onse:
Tulutsa pamodzi ndi iwe zamoyo zonse zili ndi iwe za nyama zonse, zouluka, ndi zinyama, ndi zokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi; kuti ziswane padziko lapansi, zibalane, zichuluke padziko lapansi.
Nakamba za mitengo, kuyambira mkungudza uli ku Lebanoni kufikira hisope wophuka pakhoma; anakambanso za nyama ndi mbalame ndi zinthu zokwawa pansi ndi za nsomba.
Pakuti pali munthu wina agwira ntchito mwanzeru ndi modziwa nadzipinduliramo; koma adzapereka gawo lake kwa munthu amene sanagwirepo ntchito. Ichinso ndi chabe ndi choipa chachikulu.
Zonse zoyenda chafufumimba, ndi zonse za miyendo inai, kapena zonse zokhala nayo miyendo yambiri ndi zokwawa zonse zakukwawa pansi, musamazidya; popeza ndizo zonyansa.
Musamadzinyansitsa ndi chokwawa chilichonse chakukwawa, musamadzidetsa nazo, kuti mukadziipse nazo.
satumikiridwa ndi manja a anthu, monga wosowa kanthu, popeza Iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse;