Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 1:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo Mulungu anapanga thambo, nalekanitsa madzi anali pansi pathambolo ndi madzi anali pamwamba pathambolo; ndipo kunatero.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo Mulungu anapanga thambo, nalekanitsa madzi anali pansi pa thambolo ndi madzi anali pamwamba pa thambolo; ndipo kunatero.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Motero Mulungu adalenga cholekanitsa madzi chija, naŵagaŵa madziwo, ena pansi pa cholekanitsacho ena pamwamba pake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Ndipo Mulungu anapanga thambo nalekanitsa madzi amene anali pansi ndi pamwamba pa thambo lija, ndipo zinachitikadi.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 1:7
15 Mawu Ofanana  

Mulungu ndipo anati, Dziko lapansi limere udzu, therere lobala mbeu, ndi mtengo wazipatso wakubala zipatso monga mwa mtundu wake, momwemo muli mbeu yake, padziko lapansi: ndipo kunatero.


Zikhale zounikira m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire padziko lapansi; ndipo kunatero.


Ndipo adati Mulungu, Dziko lapansi libale zamoyo monga mwa mitundu yao, ng'ombe, ndi zokwawa, ndi zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao: ndipo kunatero.


Ndipo Mulungu analitcha thambolo Kumwamba. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachiwiri.


Ndipo anati Mulungu, Madzi a pansi pakumwamba asonkhane pamodzi pamalo amodzi, uoneke mtunda: ndipo kunatero.


Amanga madzi m'mitambo yake yochindikira; ndi mtambo sung'ambika pansi pake.


Atumiza akasupe alowe m'makwawa; ayenda pakati pa mapiri:


Amene analenga zakumwamba mwanzeru; pakuti chifundo chake nchosatha.


Mlemekezeni, m'mwambamwamba, ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo.


Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake.


Usana ndi usana uchulukitsa mau, ndipo usiku ndi usiku uonetsa nzeru.


Mitambo ikadzala mvula, itsanulira pansi; mtengo ukagwa kumwera pena kumpoto, pomwe unagwa mtengowo udzakhala pomwepo.


Ndipo anazizwa anthuwo nanena, Ndiye munthu wotani uyu, pakuti ngakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa