Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 1:22 - Buku Lopatulika

22 Mulungu ndipo anadalitsa zimenezo, nati, Zibalane, zichuluke, zidzaze madzi a m'nyanja, ndi mbalame zichuluke padziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Mulungu ndipo anadalitsa zimenezo, nati, Zibalane, zichuluke, zidzaze madzi a m'nyanja, ndi mbalame zichuluke pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Adazidalitsa ponena kuti, “Swanani ndipo mudzaze nyanja, mbalamenso ziswane pa dziko.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Mulungu anazidalitsa nati, “Muswane, ndi kudzaza mʼmadzi a mʼnyanja, ndipo mbalame zichuluke pa dziko lapansi.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 1:22
16 Mawu Ofanana  

Mulungu ndipo adalenga zinsomba zazikulu ndi zoyendayenda zamoyo zakuchuluka m'madzi mwa mitundu yao, ndi mbalame zamapiko, yonse monga mwa mtundu wake: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.


Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu.


Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.


Ndipo Labani anati kwa iye, Ngatitu ndikapeza ufulu pamaso pako, ukhale, chifukwa ndazindikira kuti Yehova wandidalitsa ine chifukwa cha iwe.


Chifukwa ndisadafike ine, iwe unali nazo zowerengeka, ndipo zachuluka zambirimbiri; Yehova wakudalitsa iwe kulikonse ndinayendako: tsopano ndidzamanga liti banja langa?


Ndipo Mulungu anati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse: ubale, uchuluke; mwa iwe mudzatuluka mtundu ndi gulu la mitundu, ndipo mafumu adzatuluka m'chuuno mwako;


Tulutsa pamodzi ndi iwe zamoyo zonse zili ndi iwe za nyama zonse, zouluka, ndi zinyama, ndi zokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi; kuti ziswane padziko lapansi, zibalane, zichuluke padziko lapansi.


Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, nati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.


Tapenya tsono mvuu ndinaipanga pamodzi ndi iwe, ikudya udzu ngati ng'ombe.


Ndipo Yehova anadalitsa chitsiriziro cha Yobu koposa chiyambi chake, ndipo anali nazo nkhosa zikwi khumi ndi zinai, ndi ngamira zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi ng'ombe zamagoli chikwi chimodzi, ndi abulu aakazi chikwi chimodzi.


Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake, ndi zodabwitsa zake za kwa ana a anthu!


Ndipo awadalitsa, kotero kuti achuluka kwambiri; osachepsanso zoweta zao.


Mkazi wako adzanga mpesa wopatsa m'mbali za nyumba yako; ana ako adzanga timitengo ta azitona pozinga podyera pako.


Madalitso a Yehova alemeretsa, saonjezerapo chisoni.


Ndipo ndidzatembenukira kwa inu, ndi kukubalitsani, ndi kukuchulukitsani; ndipo ndidzakhazika chipangano changa ndinapangana nanucho.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa