Poyamba, ndiyamika Mulungu wanga mwa Yesu Khristu chifukwa cha inu nonse, chifukwa kuti mbiri ya chikhulupiriro chanu idamveka padziko lonse lapansi.
Filemoni 1:4 - Buku Lopatulika Ndiyamika Mulungu wanga nthawi zonse, ndi kukumbukira iwe m'mapemphero anga, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndiyamika Mulungu wanga nthawi zonse, ndi kukumbukira iwe m'mapemphero anga, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukira m'mapemphero anga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakukumbukira iwe mʼmapemphero anga. |
Poyamba, ndiyamika Mulungu wanga mwa Yesu Khristu chifukwa cha inu nonse, chifukwa kuti mbiri ya chikhulupiriro chanu idamveka padziko lonse lapansi.
Tiyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu nonse, ndi kukumbukira inu m'mapemphero athu;
Tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale, monga kuyenera; pakuti chikhulupiriro chanu chikula chikulire, ndipo chichulukira chikondano cha inu nonse, yense pa mnzake;
Ndiyamika Mulungu, amene ndimtumikira kuyambira makolo anga ndi chikumbumtima choyera, kuti ndikumbukira iwe kosalekeza m'mapemphero anga,
pakumva za chikondi chako ndi chikhulupiriro uli nacho chakulinga kwa Ambuye Yesu, ndi kwa oyera mtima onse;