Indedi Mulungu adzaphwanya mutu wa adani ake, pakati pamutu pa iye woyendabe m'kutsutsika kwake.
Eksodo 9:2 - Buku Lopatulika Pakuti ukakana kuwalola amuke, ndi kuwagwira chigwiritsire, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti ukakana kuwalola amuke, ndi kuwagwira chigwiritsire, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ukakananso kuŵalola kuti apite, ndi kuŵaletsa ndithu, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ngati ukana kuti apite ndi kupitiriza kuwaletsa, |
Indedi Mulungu adzaphwanya mutu wa adani ake, pakati pamutu pa iye woyendabe m'kutsutsika kwake.
Ndipo ndanena ndi iwe, Mlole mwana wanga amuke, kuti anditumikire Ine; koma wakana kumlola kuti asamuke; taona, Ine ndidzamupha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba.
Ndipo pambuyo pake Mose ndi Aroni analowa nanena ndi Farao, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Lola anthu anga apite, kundichitira madyerero m'chipululu.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uka nulawire mammawa, nuime pamaso pa Farao, nunene naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, akanditumikire.
taona, dzanja la Yehova lidzakhala pa zoweta zako za kubusa, pa akavalo, pa abulu, pa ngamira, pa ng'ombe, ndi pa zoweta zazing'ono ndi kalira woopsa.
koma ngati mukana ndi kupanduka, mudzathedwa ndi lupanga; chifukwa m'kamwa mwa Yehova mwatero.
koma kwa iwo andeu, ndi osamvera choonadi, koma amvera chosalungama, adzabwezera mkwiyo ndi kuzaza,
Ndipo anatenthedwa anthu ndi kutentha kwakukulu; ndipo anachitira mwano dzina la Mulungu wokhala nao ulamuliro pa miliri iyi; ndipo sanalape kuti amchitire ulemu.