Chifukwa chake wamkulu ndi Inu Yehova Mulungu, pakuti palibe wina wofanana ndi Inu, palibe Mulungu winanso koma Inu, monga mwa zonse tinazimva ndi makutu athu.
Eksodo 8:10 - Buku Lopatulika Ndipo anati, Mawa. Nati Mose, Kukhale monga mau anu, kuti muziwe, kuti palibe wina wonga Yehova Mulungu wathu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati, Mawa. Nati Mose, Kukhale monga mau anu, kuti muziwe, kuti palibe wina wonga Yehova Mulungu wathu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Farao adati, “Maŵa.” Apo Mose adati, “Zidzachitika monga momwe mwaneneramu, ndipo mudzadziŵa kuti palibe Mulungu wina wofanafana ndi Chauta, Mulungu wathu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Farao anati, “Mawa.” Mose anamuyankha kuti, “Chabwino zidzakhala monga mwaneneramu, kuti mudzadziwe kuti palibe wina wofanana ndi Yehova Mulungu wathu. |
Chifukwa chake wamkulu ndi Inu Yehova Mulungu, pakuti palibe wina wofanana ndi Inu, palibe Mulungu winanso koma Inu, monga mwa zonse tinazimva ndi makutu athu.
Yehova, palibe wina wonga inu, palibenso Mulungu wina koma Inu; monga mwa zonse tazimva m'makutu mwathu.
Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba padziko lonse lapansi.
Afanana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera, woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa?
Koma Mose anati kwa Farao, Ulemu ndi wanu, wa ine ai; ndipembere inu ndi anyamata anu ndi anthu anu liti, kuti aonongeke achulewo, achokere inu ndi nyumba zanu, atsale m'mtsinje mokha?
Pakuti nthawi ino ndidzatuma miliri yanga yonse pamtima pako, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako; kuti udziwe kuti palibe wina wonga Ine padziko lonse lapansi.
Ndipo Mose ananena naye, Potuluka m'mzinda ine, ndidzakweza manja anga kwa Yehova; mabingu adzaleka, ndi matalala sadzakhalaponso; kuti mudziwe kuti dziko lapansi nla Yehova.
Mudzafanizira Mulungu ndi yani tsopano, kapena kumyerekeza ndi chithunzithunzi chotani?
Kumbukirani zinthu zoyamba zakale, kuti Ine ndine Mulungu, ndipo palibenso wina; Ine ndine Mulungu, ndipo palibenso wina wofanana ndi Ine;
Ambuye Yehova, mwayamba Inu kuonetsera mtumiki wanu ukulu wanu, ndi dzanja lanu lamphamvu; pakuti Mulungu ndani m'mwamba kapena padziko lapansi wakuchita monga mwa ntchito zanu, ndi monga mwa mphamvu zanu?
Palibe wina ngati Mulungu, Yesuruni iwe, wakuyenda wokwera pathambo, kukuthandiza, ndi pa mitambo mu ukulu wake.
Potero dziwani lero lino nimukumbukire m'mtima mwanu, kuti Yehova ndiye Mulungu, m'thambo la kumwamba ndi padziko lapansi; palibe wina.
inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.